Katswiri othamanga Shantel Davie akonza mijigo yoonongeka


Ngati njira imodzi yoonetsetsa kuti mzika za dziko lino zikumwa madzi a ukhondo komaso kupeza madziwa mosavuta, katswiri ochita masewero othamanga m’boma la Mulanje Shantel Davie pa 16 ndi pa 17 mwezi uno anazipeleka kuthamanga mtunda otalika makilomita zana imodzi ndimakumi atatu ( 130) kuti akufuna kwabwino amuthandize ndithandizo landalama zokwana K1.5 miliyoni.

Mwamwayi, Katswiri oyimba mdziko la America Mary Davidson ataona ena mwamauthenga ofuna thandizoli kudzela mnyumba zolemba ndikufalitsa nkhani mdziko muno anazipeleka kupeleka ndalama yonse yomwe Katswiri othamangayu amafuna kuti agwiritse muncthito zake zachifundozi.

Pakanalipano, anthu okhala m’midzi ya Kachingwe mfumu Yayikulu Chikumbu komaso Tonya mfumu yayikulu Mkanda ndi osangalala ndikukonzedwa kwa mijigo m’madera awo yomwe yakhala zaka zambiri isakugwira ntchito.

Poyankhula ku khwimbi la anthu okhala m’mudzi wa Kachingwe omwe anasonkhana kudzachitira umboni kutsekulidwa kwa mjigo omwe wakonzedwa utatha zaka zinayi osakugwira ntchito, Shantel anati iye amamva chisoni akamaona anthu akuvutika pomwe ena ali ndiluso lomwe litha kupulumutsa miyoyo kumavuto osiyanasiyana.

Iye anati amayamika Mulungu pomupatsa luso lothamanga lomwe ndimdalitso ngakhalenso kwa ena.

“Ndimayamika Mulungu pondipatsa luso lothamanga lomwe anandipatsa. Nditakhala pansi ndinaona kuti lusoli lisakhale thandizo pa ine ndekha komanso likhale thandizo kwa ena omwe ali osowekedwa. Ndichifukwa chake lero ndilipano kutsekulira mjigo omwe ndakonzetsa kudzera mulusoliri,” anatero Shantel.

Shantel anati anali okhudzidwa kwambiri pomwe khansala wadelari amakapeleka pempho lake lofuna chithandizo chamjigo.

Iye anaonjezera anthu m’mudzi wa mfumu Kachingwe akumayenda mitunda italiitali kuti apeze madzi akumwa komanso ogwilitsira ntchito zosiyanasiyana zapakhomo kotero kuti anachiona chamtengo wapatali kuti athandize vutoli kudzera muluso lake lothamanga.

” Ine monga munthu yemweso ndakhala munyengo zamavuto ngati awa, ndinali okhudzidwa pomwe akhansala adera lino amakandiuza zavutoli kuti ndithandizepo atamva zina mwantchito zachifundo zomwe ndakhala ndikugwira kudzera muluso langa lothamangali. Ndichifukwa chake ndinati ndisazengeleze koma ndipeze anthu akufuna kwabwino nawalonjeza kuti nditha kuthamanga mtunda umenewu kuti andithandize ndindalama zogulira zipangizo zokhonzetsera mjigowu. Mwamphamvu ya Mulungu, ndalama inapezeka yomwe takonzetsera mjigo ukutsekulidwa lelowu. Ndikuthokoza mayi Mary Davidson omwe atithandiza ndi ndalama zokhonzetsera migoyi,” anatero Shantel.

Katswiriyu anapempha ena omwe alindimaluso osiyanasiyana kuti asamangodyelera paokha maluso omwe alinawowa koma kuti azithandizanso ena omwe alibe maluso ngati awa ndipo akukumana ndimavuto osiyanasiyana.

Iye anatsindikanso kuti ndiokonzeka kuthamanganso mtunda wawutali ndicholinga chofuna kupeza thandizo landalama zogulira chimanga chomwe azachigawe m’maanja ovutika omwe pakadali pano akuvutika ndinjala.

“Ndinalandira madandaulo awiri pakamodzi, lanjala komanso madzi. Ndinachiowona chamtengo wapatali kuyamba kukonza vuto lamadzi lomwe lakhala zaka zochuluka. Panopa ndili okonzeka kuthamanganso mtunda wautali kuti ndipeze ndalama zogulira chimanga chomwe ndizagawe kumaanja ovutika omwe panopa akuvutika ndinjara. Choncho, ndikufuna akufuna kwabwino andithandize ndipo ndili okonzeka kuthamanga,” anatero Shantel.

M’mawu ake, mfumu Chathu omwe ndim’modzi mwamafumu ozungulira mfumu Kachingwe ndipo akhala akugwilitsanawo ntchito mjigowu, anati iwo ndiokondwera ndikukokozedwa kwamjigowu omwe tsopano ukhale ukuwapezetsa madzi awukhondo komaso mosavuta.

“Tili osangalala kwambiri ndikukonzedwanso kwa mjigo umenewu umene watha zaka zinayi usakugwira ntchito. Tili ndichikhulupiliro kuti tsopano matenda odza kamba komwa madzi osakhala bwino achepa. Tikhala tikumwa madzi awukhondo tsopano. Pachifukwa ichi,tikumuthokoza Shantel chifukwa cha ntchito zake zachifundo ndipo apitilize kotelo m’midzi ina yozungulira komwe kulinso mavuto onga awa,” anatero mfumu Chathu.

Pothirapo ndemanga, m’modzi mwa amayi omwe akhale akugwiritsa ntchito mjigowu mayi Akometse Mofati anati iwo monga mzimayi ndiokondwa ndikukonzedwanso kwa mjigowu omwe akuti tsopano uwachepetsela ntchito yoyenda mitunda italiitali kukafufuza madzi abwino.

” Tili osangalala kwambiri ndikukonzedwanso kwa mjigo umenewu. Kwazaka zinayi zomwe mjigowu unali chionongekereni, takhala tili pamavuto ochuluka monga matenda otsekula m’mimba komanso kuyenda mitunda italiitali kusakasaka madzi akumwa. Tikumuthokoza Shantel chifukwa cha ntchito yotamandika yomwe akugwira. Mulungu apitilize kumudalitsa,” anatero mayi Mofati.

Kupatula kukonza mijigo iwiriyi, Shantel anapelekanso chimanga ndizakudya zina kwa maanja ovutika m’dera lamafumu awiriwa.

Pakadalipano, Shantel akukonzanso zothamanga mtunda wautali kuti apeze ndalama zopangira phwando lachisangalaro cha khilisimisi Komanso chaka chatsopano ndi ena mwa ana ochokera m’maanja ovutika.