Mbama yoyera: Papa akuntha mzimayi

Advertisement

Papa Francis anakuntha dzanja la mayi wina yemwe anamukoka Papayo ku chisangalalo cha chaka chatsopano ku St. Peters Square.

Izi zinachitika lachiwiri Papa, yemwe ndi mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse, atangomaliza kumupatsa moni mwana wina.

Mayiyo anagwila ndikukakamila dzanja la papa kwakanthawi ndipo Papa anayesera kuzichotsa koma mayiyo anakakamira.

Izi zinakwiyitsa Papa ndipo anathibula dzanja la mayiyo.

Izi zinakwiyitsa akhilisitu ambiri ndipo popereka mafuno abwino a chaka cha tsopano kwa anthu ku St Peters Square, Papa analapa posaugwila ntima ndikuthibula dzanja la mayiyu lachiwiri usiku.

“Chikondi chimatipangitsa ife kukhala odekha, nthawi zinaso timatha osaugwila mtima- chimodzi modzi ineso. ndipo ndikupepesa pa chitsanzo choyipa chomwe ndidaonetsa zulo,” anatero Papa.

 

 

 

Advertisement