Ndinapita kumwamba, ndili ndi digiri yamachilitso – watero bambo wina

Advertisement

Bambo wina wa m’boma la Dowa wadabwitsa anthu ponena kuti anapita ku sukulu yaukachenjede yakumwamba komwe anapatsidwa digiri ya machiilitso.

Bamboyu yemwe wati anapita kumwamba mchaka cha 2015, ndiwazaka makumi asanu ndilimodzi ndiso mphambu zisanu (65) ndipo dzina lake ndi Notice Chafumbula ochokera m’mudzi mwa Kafula muboma lomweli la Dowa.

Chafumbula akuti anaonekeredwa ndimngelo yemwe anamutenga kupita naye kumwamba kwa mulungu komwe anauzidwa ndi mulungu mwini kuti akufuna amupatse mkuluyu zinthu zake zomwe analengedwera.

Mkuluyu wati apa mulungu anamupititsa ku sukulu ya ukachenjede chotchedwa Chescori Sasa Somiley komwe pakutha pamaphunziro kwa masiku angapo anapatsidwa ma digiri okwana 191 ndipo imodzi mwa iwo inali yochilitsa matenda osiyana siyana.

“Ndinkasala kudya komaso kupemphera pa phiri linalake pomwe mngelo anandionekera ndikunditenga ine kupita nane kumwamba komwe mulungu anadiuza kuti akufuna andipatse zomwe anandilengera.

“Ndinaphunzitsidwa kwa masiku asanu ndi atatu (8) ndipo pamapeto pake anandipatsa ma digiri 191 ndipo imodzi mwaiwo inali yochilitsa matenda osiyanasiyana,” watelo Chafumbula.

Apa mkachenjede wakumwambayu anati padziko lonse lapansi pali matenda okwanira mazana asanu ndi awiri, makumi anayi, mphambu zisanu ndi ziwiri (747) omwe anati malingana ndimaphuziro omwe analandira kumwambako, iye amachilitsa onsewa.

A Chafumbula anati iwo akumachilitsa anthu ochuluka omwe akhala akuchitira umboni zamachilitso awo ndipo ati akumachilitsaso angakhale anthu opanda chikhulupiliro kaamba koti iwo ndi mwana wamulungu choncho samachita tsankho.

“Ndimachilitsa ngakhale awo amene alibe chikhulupiliro chifukwa choti ndine mwana wa mulungu ndipo sindimasewera. Ndimapita mumzipatala komwe ndikangokhudza odwala, mulungu amayankhula pompo pompo.

Munthu wa Mulungu yu anati ma digiri ena omwe wapatsidwa ndi mulungu ndimonga; odziwa komaso kutanthauzila zilankhulo za mulungu, yodziwa nzeru ya mulungu ndipo iyi imatchedwa Crisoria yomwe anati imathandiza munthu kupanga chilichose pongogwiritsa ntchito mawu.

Bambo wa ku Dowayu anatiso pomwe anali kumwambako, mulungu anamulowetsa mufakitale ya golide komwe anamuumbaso ndipo anapatsidwa mphamvu zochotsa azitsogoleri mmaudindo, kupha ndi mawu ngakhaleso kuononga mapiri.

Izi zikubwera patangotha masiku angapo pomwe bambo wina posachedwapa anazitcha kuti iye ndi mulungu ndipo anthu amumpingo mwake akumamulambira.

Bamboyu yemwe dzina lake ndi Overtone Makuta akuti anakhala mulungu mchaka cha 2016 pomwe mzimu unalowa mu mtima mwawo ndipo anabadwaso mwatsopano kotero kuti sakuona zachilendo kuti anthu azimugwadira ndi kumulambira

Advertisement