Zamasiku omaliza: Munthu azitchula kuti ndi mulungu

Advertisement

Pomwe bukhu lopatulika limafotokoza bwino zomwe zizachitike masiku omaliza, bambo wina akuzitcha kuti iye ndi mulungu ndipo anthu a mumpingo mwake akumamulambira.

Bamboyu yemwe dzina lake ndi Overtone Makuta wati iyeyo ndi mulungu kotero kuti sakuona zachilendo kuti anthu azimugwadira ndi kumulambira.

A Makuta omwe anayankhula ndiimodzi mwa wailesi mdziko muno anati iwo anakhala mulungu m’chaka cha 2016 pomwe ati Yesu Mkhristu analowa mu mtima mwawo ndipo anabadwaso mwatsopano.

Iwo anati monga bukhu la mawu a Mulungu limanenera, aliyese amene Yesu wamulowa dzina lake limasintha ndipo amakhala mwana wa Mulungu ndipo wati ndi chifukwa chake naye wasintha dzina kukhala ‘Ambuye’ Overtone Khristu Makuta.

Mkuluyu anapelekera chitsanzo cha nthawi yomwe Yesu Mkhristu anali pa dziko lapansi kuti dzina lake anali Yesu Yosefe ndipo chifukwa choti Yesu analowedwa ndikumagwiritsidwa ntchito ndi Yehova, dzina lake linasintha ndipo anakhala Ambuye Yesu Yosefe Mkhristu.

Apa ‘ambuye’ Makuta anati sakuona chovuta kuti anthu amumpingo mwawo akumutchula iye kuti mulungu ponena kuti naye wapanga zomwe zinachitika pa Yesu Mkhristu nthawi yomwe anali padziko lapansi.

“Inetu sindikuona vuta chifukwa Yesu naye anapanga zomwezi komaso ngati munthu umayenera kutenga dzina la bambo ako ndipo ngati ukugwiritsidwa ntchito ndi Mulungu dzina lako limayenera lisinthe komaso ineyo ngati dzina lawo ali mulungu, naneso ndikuyenera kutenga dzina lomwelo,” anatero a  Makuta.

Kupatula zomwe wayankhula pa wailesizi, kanema yemwe akuonetsa mamembala ampingo wa mkuluyu akulambila komaso kumutchula kuti mulungu ali ponseponse pa masamba amichezo pa intaneti.

M’makanemawa, otsatila amkuluyu akuoneka akuyala nsalu zawo pansi kuti mkuluyu asaponde dothi pomwe akuyenda ndipo ena pomwepo amamutchula kuti mulungu ena amati mulengi.

M’modzi mwa akuluakulu ampingo wa ‘ambuye’ Makuta ‘mulungu’ wa m’boma la Ntchisi wati anthu omwe sanakumanepo ndi mkuluyu ndi atsoka ponena kuti akusemphana ndi chipulumutso chawo.

Mkuluyu wati ndizovetsa chisoni kuti mulungu wabweraso kudzera mwa a Makuta koma anthu akubweleza zolakwika zomwe anachita make dzana pomukana Yesu Mkhristu ndipo ndizokhumudwitsa kuti anthu akuwaona ambuye Makuta ngati ndi munthu mzawo.

Akulu ampingowa achemelera a Makuta kuti ndi mulungu weniweni ndipo anati akalankhula chinthu chikumakhala chomwecho komaso kuti akusintha miyoyo ya anthu ochuluka ndipo wapempha mulungu wawoyu kuti ayende mmadera ambiri kuti asinthe miyoyo yochuluka.

 

Advertisement