Mwana apha make tsiku la anakubala

Advertisement
Police

Mnyamata wina yemwe akuganizilidwa kuti ndi wamisala wapha mayi ake tsiku la anakubala m’boma la Chitipa kaamba kokana kugona naye.

Izi ndimalingana ndi mneneri wa apolisi m’bomali a Gladwel Simwaka omwe azindikila mnyamatayu ngati Elisha Kapira wazaka 29 yemwe wapha mayi ake a Edris Nakabala azaka 59.

A Simwaka ati mai ndi mwanayu onse amakhalira limodzi m’dziko la Zambia ndipo anabwera ku Nthalire m’bomali ndi cholinga choti adzaone azibale awo komaso kuti adzaone pomwe anaikidwa amunawo omwe amwalira miyezi yapitayo.

Atafika mdera lawoli, abale awo anawapatsa anthuwa nyumba kuti adzikhalira limodzi posaganizira kuti zinthu zamtunduwu zingachitike.
M’bandakucha wapa 15 Okutobala, tsiku lomwe anthu mdziko muno amakumbukira anakubala, mwanayu anawauza mayi akewa kuti akufuna agonane nawo.

Izi zinadzetsa tsembwe kwa amayiwa omwe samayembekezera kumva zinthu zamtunduwu kuchokela kwa chipatso cha mchiuno mwawo momwe ndipo amayiwo anatemetsa nkhwangwa pamwala kuti sangapange malodzawo.

Malingana ndi apolisi, izi zinakhumudwitsa mwanayo yemwe anatenga mpeni ndikuyamba kuwabaya mayi akewo ndipo mayiyo anafera malo angozi omwewo.

Apa apolisi a pa Nthalire sanachedwe koma kuthamangira kumalo omwe izi zinachitikila ndipo anamanga oganizilidwayu komaso kutengera kuchipatala thupi la malemuwa.

Malingana ndi zotsatira za kuchipatala, imfayi inabwera kaamba koti mayiyu anataya magazi ochuluka komaso kuti anali ndi mabala ochuluka mmutu mwawo.

Pakadali pano apolisi ati atengera Elisha kuchipatala kuti akamuyeze ngati alidi wamisala.

Advertisement