Kongelesi sidzalamuliranso Malawi, watero Mutharika


Mtsogoleri wa dziko lino, Peter Mutharika, wanenetsa kuti chipani chotsutsa cha Malawi Congress (MCP) sichidzalamuliraso dziko lino.

Mutharika: sadzalamuliranso

A Mutharika alankhula izi posachedwapa pomwe amayankhula ndi imodzi mwa wailesi za kanema zodziwika bwino pa dziko lonse ya Aljazeera.

Mtsogoleri wa dziko linoyu anati sizizathekaso kuti a Malawi mkuzavoteraso chipani cha MCP ponena kuti a Malawi anaipidwa ndi ulamuliro wa chipanichi ndipo ndikosatheka anthu kuzavoteraso chipanichi mutsogolo muno.

A Mutharika anati chipani cha MCP chinanzunza anthu ochuluka mdziko muno kwa zaka makumi atatu ndi mphambu imodzi (31) muulamuliro wa mtsogoleri oyamba wadziko lino a Kamuzu Banda zomwe anthu sanaiwalebe.

Iwo anati chipanichi chizakhalabe chipani chotsutsa mpaka kalekale kaamba koti anthu anada nacho kukhosi.

“Chipani cha Malawi Congress chinadziwika bwino ndi kupha, anthu kusowa, anthu kuponyeredwa m’mitsinje ku adyedwe ndi ng’ona ndiye anthu amakhala akukumbukabe zosezi sanaziiwale.

“Sizingathekeso panopa ndipo ndikukitsimikizilani, a Malawi sangavoteleso chipani cha Malawi Congress ndipo ichi ndi chifukwa chake chipanichi chalephera pa zisankho zisanu ndi chimodzi zapitazi (6),” anatero Mutharika.

Mtsogoleriyu ananenaso kut ndizokhumudwitsa kuti chipanichi mpaka lero sichikuvomeleza kuti chinalephera zisankho za pa 21 May chaka chino ndipo iwo anati izi ndikaamba koti chipani chikufunitsitsa chitalamula dziko lino zomwe ndi zosatheka.

Apa a Mutharika anauza wailesi ya kanemayi kuti iwo ndiomwe anapambana pa zisankho zapitazi ndipo zisankhochi chinayenda mopanda chinyengo chilichose.

A Mutharika anati mabungwe akuluakulu padziko lonse omwe amagwira ntchito mosakondera mbali, anaonelera chisankhochi ndipo anapeza kuti panalibe chinyengo ndipo anati ndizodabwitsa kuti chipani cha MCP chikutsutsabe zotsatirazi mpaka pano.

“Chisankhochi chinayenda bwino opanda mavuto ndipo azipani zotsutsa analephera zisankhozi koma asankha kusavomereza zotsatilazi ndipo akubweletsa chisokonezo mdziko muno,” anaonjezera a Mutharika.

Pakadali pano nkhani yazotsatira za zisankho za mtsogoleri wadziko inakalibe ku khothi ndipo kumamaliziro kwa chaka chino bwalo likuyembekezereka kuzalamula ngat pakhale zisankho zina kapena ayi malingana ndi pempho la chipani cha MCP.

4 thoughts on “Kongelesi sidzalamuliranso Malawi, watero Mutharika

  1. Dpp isiyeni yilamulile mwatendele anthu woyipa inu zimufuna kugonja munaludza basi Dpp paka 2080 cheeeee

  2. Pitala ndi mwana wa hule saziwa kumene anachokera , zimene amafuna iye nkuononga mitundu wa a Malawi …
    Chifukwa iye sali Citizen wa Malawi

  3. Dikila chipani chakochi chidzatha ngati UDF watch and see

  4. Mutharika seems as if he is ignorant, People will vote MCP because the leadership that was bad is gone long time now is another generation of leadership.
    People knows that,so dont waste your time thinking that people will not vote for MCP ,what you must do is to stop rigging election votes and again stop using tippex.

Comments are closed.