Namadingo alowera ku bibida

Nkhani yomwe inamanga nthenje mu sabata langothali ndiyokhudza katswiri oyimba nyimbo za uzimu Patience Namadingo.

Bambo Namadingo ndi amene anayendesa mwambo okhadzikisa chakumwa cha ukali chomwe akufulura a kampani ya Castel, lachisanu lapitali. Ndipo Ku mwambowu kudali gulu lochokera mu dziko la Kenya la Sauti Sol.

Izi zadabwitsa a Malawi ambiri potengera kuti Patience ndi munthu ofalisa uthenga wa uzimu, ndipo za uzimu zidasemphana ndi mowa. Koma ena amumvetsetsa poganizira kuti kanganyase kali pa minga.

Katswiriyu, kupatula kuimba mwanthetemya, alinso ndi Mphatso yopanga zisudzo. Choncho, mkutheka kuti kampani ya Castel inatengela luso limeneli kuti ampase ntchito yo.

Namadingo anadziwika mu chaka cha 2010 ndimayimbidwe ake okoma omwe adaonekera mu nyimbo ya Mtendere. Kufikira tsiku la lero, adakali odziwika mu utumikiwu.

Advertisement