DPP sikanawina popanda ine – atero a Chilima

Advertisement

Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino a Saulos Chilima ati iwo ndi omwe anapangitsa kuti chipani cha Democratic Progressive chipambane zisankho za m’chaka cha 2014 ndiye chipanichi chisiye kuwasokosa.

Chilima: ndisamveso zachibwana

A Chilima ananena izi dzulo pomwe anapangitsa msonkhano wa chipani chawo cha UTM pa bwalo la sukulu ya pulaimale ya Chule ku Dedza.

Iwo amayankhapo pa zomwe atsogoleri a DPP akhala akunena kut a Chilima anali munthu osadziwika pomwe mtsogoleri wa dziko lino a Peter Mutharika ankawatenga kuti akhale wachiwiri wawo mu 2014 ndiye akuyenera azithokoza chipanichi.

Koma a Chilima anati iwo sakuyenera kuthokoza aliyense kupatula Mulungu popeza atsogoleri a DPP ndi omwe anawapeza ku ofesi kwawo mu 2014 kuwapempha kuti asiye ntchito yawo yabwino ndi kulowa ndale.

A Chilima anaonjezera ku chipani cha DPP anachipeza chili chotsutsa ndipo zinatengera ukadaulo wawo kuti chipanichi chilowe mu boma.

“Zomatitenga ngati anthu opemphetsa, anthu osayamika zimenezo zitheretu. Chifukwa amene amayenera kuyamika mzake ndi inuyo. Simukanawina inu a DPP chipanda enafe kukuthandizani, ndiye musamatisokose iyayi,” anatero a Chilima.

Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko linoyu ananetsanso kuti sangatule pansi udindo wake chifukwa ntchito yomwe analembera mu 2014 itha mu 2019.

“Ikanakhala kuti 2019 yakwana ndiye tikuumilira kupitiliza iyo ndi nkhani yapadera, ndisamveso zachibwana,” anatero a Chilima molalata.

A Chilima anatuluka chipani cholamula cha DPP mu June chaka chino ndipo anayambisa chipani cha UTM. Iwo akuyembekezeka kuzapikisana ndi a Mutharika ndi ena pa zisankho za mtsogoleri wa dziko lino chaka cha mawa.

Advertisement

One Comment

  1. Hahahaha zopusa basi….ndie ngat inu munawinitsa Dpp.. Now is your turn pangani zot muwine ”!!!

Comments are closed.