…wakana anyamata awiri omwe anafa pangozi…
Mneneri odziwika bwino Shepherd Bushiri wati zamukwana komaso zamutopetsa zitonzo zomwe akulandira.
Bushiri wanena kuti ndiwokhumudwa kwambiri ndi zitonzo zomwe akumuchitira anthu m’Malawi muno.
Bushiri yemwe ndi mwini wake wa tchalitchi cha Enlightened Christian Gathering (ECG) wati asiya kuthandiza a Malawi ku utumiki wake.
Iye amayankhula izi kudzera kwa omuyankhulira wake Ephraim Nyondo yemwe watsindika kuti athamangisa a Malawi ochulukirapo kuti asamugwilireso ntchito kaamba koti anthu ochuluka kuno kumudzi sakuyamikira pazabwino zomwe iye amachita.
“Bushiri akuchita zinthu zambiri zopindulira a Malawi koma ndizodabwitsa komaso zodzetsa tsembwe kuti anthu ambiri akumunyoza kwambiri ndipo akumutenga ngati chigawenga.
“Iye amathandiza a Malawi ambiri Ku South Africa koma palibe yemwe amabwera poyera ndikuyamika za zimenezi. Komano choipa china chake chikangochitika kwa anthuwo, anthu mdziko muno amamuda Bushiri,” a Nyondo anatero.
Chatsitsa dzaye kuti njobvu ithyoke mnyanga ndi imfa ya anyamata atatu omwe ankamugwilira ntchito ndipo onse amwalira milungu iwiri yapitayo pangozi yagalimoto pomwe amachokera Ku msonkhano wa mneneriyu ku Lilongwe kunka Ku South Africa.
Anyamatawa omwe ndi James Nee, Beston Khamba ndi Brain Gondwe anafera pamalo pangozipo galimoto yomwe anakwera paulendo wawo itaombana ndi galimoto yamtundu wa thilaki.
Ngakhale kuti Bushiri anathandiza zinthu zochuluka pa maliro a anyamata atatuwa, a Malawi ambiri akumamutoza mneneriyu pa imfayi kunena kuti akudziwapo kanthu pa za imfayi zinthu zomwe zamukhumudwisa Bushiri.
Tikunena pano mtsogoleri wa ECG yu yemwe ndimmodzi mwa anthu okhupuka mmdziko la South Africa, wati anthu akumulakwira kwabasi kumutoza za imfayi ndipo wabwera poyera kunena kuti pa anthu atatuwa yemwe amamudziwa anali James Nee yekha.
“Zonsezi sichina ayi koma imfa ya anyamatawa; James, Beston ndi Brain. Bushiri ankadziwa James (Mlambili Wa tchalitchi) yekha pa anyamata atatuwa,” watero Nyondo yemwe amayankhula m’malo mwa Bushiri.
Kukanaku kwautsa manong’onong’o ochuluka pa masamba a mchezo a fesibuku ndi WhatsApp pomwe anthu akugawana kanema owonetsa anyamatawa akugwilira ntchito mneneriyu.
Ngoziyi itangochitika kumene, Bushiri analemba pa tsamba lake la fesibuku kuzindikira anyamata omwe anatisiyawa ngati ogwira ntchito ake ndipo anati Beston ndi Brain anali ma shoveli amagalimoto ku tchalitchi chake koma lero wawakana anthuwa.