Koma amatha kulalata – Dausi asilira Chilima

Advertisement
Dausi

Kukhala ngati akulakalaka akanamupatsa u Regional Governor, mwinamwake uko luso lake likanaonekela bwino.

Mneneri wa boma amenenso ndi wamkulu mu chipani cholamula boma cha DPP a Nicolas Dausi wati wagoma ndi luso lotukwana limene a Chilima ali nalo.

Dausi
Dausi wavula chisoti.

Polankhula pa wailesi, a Dausi anati a Chilima akuyenela kutula pansi udindo chifukwa iwo sakugwilizana ndi zimene anthu a chipani cha DPP akuchita.

Pachiweru, a Chilima anakhazikitsa chipani chawo pa bwalo la Masintha mu mzinda wa Lilongwe.

Mwa zina a Chilima anati chipani cha DPP ndi cha anthu akuba ndipo akuchita kukhala ngati akankhila pumbwa ku chipwete.

Pothililapo ndemanga pa zimene zinalankhulidwa pa msonkhanowu, a Dausi anapempha kuti a Chilima atule pansi udindo.

Iwo anaonjezelapo kuti a Chilima aonetsa kuti ndi munthu wa luso lotukwana.