Koma amatha kulalata – Dausi asilira Chilima

Advertisement
Dausi

Kukhala ngati akulakalaka akanamupatsa u Regional Governor, mwinamwake uko luso lake likanaonekela bwino.

Mneneri wa boma amenenso ndi wamkulu mu chipani cholamula boma cha DPP a Nicolas Dausi wati wagoma ndi luso lotukwana limene a Chilima ali nalo.

Dausi
Dausi wavula chisoti.

Polankhula pa wailesi, a Dausi anati a Chilima akuyenela kutula pansi udindo chifukwa iwo sakugwilizana ndi zimene anthu a chipani cha DPP akuchita.

Pachiweru, a Chilima anakhazikitsa chipani chawo pa bwalo la Masintha mu mzinda wa Lilongwe.

Mwa zina a Chilima anati chipani cha DPP ndi cha anthu akuba ndipo akuchita kukhala ngati akankhila pumbwa ku chipwete.

Pothililapo ndemanga pa zimene zinalankhulidwa pa msonkhanowu, a Dausi anapempha kuti a Chilima atule pansi udindo.

Iwo anaonjezelapo kuti a Chilima aonetsa kuti ndi munthu wa luso lotukwana.

Advertisement

9 Comments

  1. Ndikupempha kuti nose a DPP muthule pansi maudindo tifuna tilowemo mwalephera apo biii tilowa mutchire

  2. Simunati inu nde muthu oipa kwambili amene sinuous an Galatea mumuyakhula ngati amalawi ndife ana anu chilima boma basi

  3. Sanati abambo amenewa alila kwambili amaganiza kuti amatha kuyakhula next year kundende

  4. Vuto chilungamu Chimawawa. Our nation needs a leader like Chilima. Mwana vomerezani our boat is sinking

  5. Wooo Dausi you’re one of the people who are in a sinking boat DPP.we’re counting down days,weeks and months 2019 is coming.

  6. Andale ndichoncho nthawi zonse safuna nzawo achite zokomera anthu

  7. Aaa a Dausi bodza , kutukwana ndkuiti apa? Mwagwa nayo a Dausi mukwera yakuphwa. Chaka chakenichino.

Comments are closed.