Zitayeni a Peter

Advertisement
Peter Mutharika

Ikuvuta kuijama iyiyi. Akanakhala a Chilima mwina akanatimasula kuti paja akakhala pa mkhate si umo avutila kupha.

A Malawi ochuluka ati Mtsogoleri wa dziko lino a Peter Mutharika atule pansi udindo wawo ndipo afufuzidwe.

Peter Mutharika
A Mutharika akupemphedwa kuti atule pansi udindo wawo.

Pa masamba a social media, anthu ochuluka ati a Mutharika sakuyenelanso kukhala otsogolera dziko lino.

Izi zayamba kunenedwa kutatuluka lipoti limene likuganizilidwa kuti ndi lochokela ku ACB losonyeza kuti a Mutharika adapindula nawo ku ndalama zakuba pa malonda amene anachitika ku Polisi.

Malinga ndi lipotili limene a ACB sanavomele kapena kukana kuti ndi lawo, mmwenye wina wa bizinesi ya Katangale adasonjola ndalama pafupifupi K500 miliyoni ku boma ndipo K145 million anaika ku account ya DPP imene osayinila ake ndi a Peter Mutharika.

Izi zatutumutsa a Malawi ambiri ndipo ochuluka akhala akupempha kuti a Mutharika atule pansi udindo.

Koma a kunyumba ya boma ati nkhani ya lipotiyi ndi ya bodza chabe.