Chipasupasu ku Manoma: Kamwendo azitaya, timu imukakamila

Advertisement
Joseph Kamwendo

Ululu wa Vita ukuzunguzabe Manoma. Mbwiza anavina Manoma ku Congo, Tchopa wa pa Bingu adakawazunguzabe a ku banja la nyerere. Inu, Vita si zibwana iyayi. Ndi izi lero Manoma ali ngati pa nsanja ya Babulo aliyense angolubwalubwa ngati oduka mutu.

Patangopita ka nthawi kochepa, Esau Kanyenda atalengeza kuti wazitaya ku Manoma, tsopano naye Joseph Kamwendo ati wazitaya naye.

Joseph Kamwendo
Joseph Kamwendo

Sabatayi yayamba mowawasa ku Manoma pamene zinaululika kuti Kamwendo amatafulila anthu ena mu timuyo kuphatikizapo a Esau Kanyenda kuti akufuna kumulanda u captain.

Izi zitachitika, Kanyenda analengeza kuti wazisiya ku Manoma. Lingaliro lake linagawa pakati anthu okonda Manoma pamene ena amaona kuti kuli kwabwino iye apite ndipo ena amaona kuti Kamwendo ndiye olakwa.

Dzulo lachitatu, Manoma analengeza kuti Kamwendo amuvula u Captain. Sipanatenge nthawi, naye Kamwendo analengeza kuti wazidomoka.

Koma wapampando wa Noma, a Gift Mkandawire wati Kamwendo samulola kupita iyayi.

Poyankhula pa wailesi, iwo ati Kamwendo ali ndi contract yofika chaka chamawa adakali ku Noma.