Mwati a Kabwila anaphunzira?

Advertisement
Jessie Kabwila

Nanthambwe wazitengela uku. Andione, andione wapezeka wakhalila zake zomwe.

A Malawi aonetsa kukwiya ndi mfundo yomwe ananena Mayi Kabwila mu nyumba ya malamulo yoti boma lisiye kuzunza a Muluzi.

Mu sabatayi Mayi Kabwila anaima mu nyumba ya malamulo ndikupempha kuti mulandu wa a Muluzi uthe. Iwo ati zaka khumi ndi mphambu ziwiri zomwe mulanduwu wakhala ukuimbidwa ndi nkhanza kwa a Muluzi.

Onjezani Kenani
a Kenani adzudzula Mayi Kabwila.

A Malawi atamva nkhani iyi anakwiyila Mayi Kabwila ndipo anabwela poyela ndikudzudzula kaganizidwe ka mayiyu.

Mlembi Onjezani Kenani ndiye anatsogolela a Malawi pa Facebook podzudzula Mayi Kabwila.

“Ndakhumudwa nanu Mayi Kabwila,” a Kenani analemba. Ndipo anapitiliza:

“Ngati a Muluzi akufuna ulemu, auzeni asiye kuzembazemba. Kuwauza kuti afotokoze za chuma chawo sikulakwa konse ndipo si nkhanza.”

Pothililapo ndemanga ife a Malawi24 titalemba nkhaniyi, a Cassim Chimuzu adanena kuti a Kabwila ndi ozweta.

“M’zimai uyu mutu wake sumayenda bwino ayi, ndipo poyamba ali ku school kuja pomwe amalimbana ndi a Bingu ndimkayesa kuti amaganiza bwino bwino komano atangobwera Ku ndale ndipamene ndidazindikira kuti sazindikila zimene akuyankhura nthawi zambiri,” iwo anatelo.

“Nanga tangoganizani momwe zinthu zafikila kunyasalande pa nkhani ya katangare wina oti akuyimira anthu pa nkhani za malamulo angamakwere pa chulu mkumati musiyeni munthu amene adawonga ndalama za amphawiyo! Aaaa dzana lomweri amabwebweta kuti Ife tikalowa m’boma tidzathetsa katangare koma sakuwona kuti akudzipaka paka? Koma Mai ameneyu ayi ndithu misala siposa apa,” anamaliza motelo a Chimuzu.

A Joel Banda anadabwa ngati Mayi Kabwila amene ndi mphunzitsi wa ku sukulu ya ukachenjede ya ku Chancellor College ndi ophunziladi.