Mwati a Kabwila anaphunzira?

Jessie Kabwila

Nanthambwe wazitengela uku. Andione, andione wapezeka wakhalila zake zomwe.

A Malawi aonetsa kukwiya ndi mfundo yomwe ananena Mayi Kabwila mu nyumba ya malamulo yoti boma lisiye kuzunza a Muluzi.

Mu sabatayi Mayi Kabwila anaima mu nyumba ya malamulo ndikupempha kuti mulandu wa a Muluzi uthe. Iwo ati zaka khumi ndi mphambu ziwiri zomwe mulanduwu wakhala ukuimbidwa ndi nkhanza kwa a Muluzi.

Onjezani Kenani
a Kenani adzudzula Mayi Kabwila.

A Malawi atamva nkhani iyi anakwiyila Mayi Kabwila ndipo anabwela poyela ndikudzudzula kaganizidwe ka mayiyu.

Mlembi Onjezani Kenani ndiye anatsogolela a Malawi pa Facebook podzudzula Mayi Kabwila.

“Ndakhumudwa nanu Mayi Kabwila,” a Kenani analemba. Ndipo anapitiliza:

“Ngati a Muluzi akufuna ulemu, auzeni asiye kuzembazemba. Kuwauza kuti afotokoze za chuma chawo sikulakwa konse ndipo si nkhanza.”

Pothililapo ndemanga ife a Malawi24 titalemba nkhaniyi, a Cassim Chimuzu adanena kuti a Kabwila ndi ozweta.

“M’zimai uyu mutu wake sumayenda bwino ayi, ndipo poyamba ali ku school kuja pomwe amalimbana ndi a Bingu ndimkayesa kuti amaganiza bwino bwino komano atangobwera Ku ndale ndipamene ndidazindikira kuti sazindikila zimene akuyankhura nthawi zambiri,” iwo anatelo.

“Nanga tangoganizani momwe zinthu zafikila kunyasalande pa nkhani ya katangare wina oti akuyimira anthu pa nkhani za malamulo angamakwere pa chulu mkumati musiyeni munthu amene adawonga ndalama za amphawiyo! Aaaa dzana lomweri amabwebweta kuti Ife tikalowa m’boma tidzathetsa katangare koma sakuwona kuti akudzipaka paka? Koma Mai ameneyu ayi ndithu misala siposa apa,” anamaliza motelo a Chimuzu.

A Joel Banda anadabwa ngati Mayi Kabwila amene ndi mphunzitsi wa ku sukulu ya ukachenjede ya ku Chancellor College ndi ophunziladi.

Advertisement

12 Comments

 1. Kabwira anabwura kale chamba cha Ku Salina ,normal person can’t say that the courts should leave Muluzi alone, the very same person says MCp will fight corruption so which is which, instead Kabwira should advice Muluzi not to run away from the courts,

 2. MCP CHIPANI CHOIPA CHASANKHO DPP CHIPANI CHAKUBA ZIWIRIZI SITIKUZIFUNASO mulandu wa chair palibepo akuba okhaokha sazengana mulandu nkumaononga ndalama za a Malawi.Kabwira sakulakwisa milandu yoseyi tilinayo yakuba ya pompano palibe tikuyakhula tizikakamba zopanda tchito 86 MPs a wapasa ngongole each 40 million kwacha yachokera kuti tonse tiliphe!!! Tizikamba za chair kupusa ife a Malawi.

 3. MCP CHIPANI CHOIPA CHASANKHO DPP CHIPANI CHAKUBA ZIWIRIZI SITIKUZIFUNASO mulandu wa chair palibepo akuba okhaokha sazengana mulandu nkumaononga ndalama za a Malawi.Kabwira sakulakwisa milandu yoseyi tilinayo yakuba ya pompano palibe tikuyakhula tizikakamba zopanda tchito 86 ministers a wapasa ngongole each 40 million kwacha yachokera kuti tonse tiliphe!!! Tizikamba za chair kupusa ife a Malawi.

 4. Tandifunsiranidi ngati mayi wa a madzidziwa zimene akulankhula.Anamudziwa mayiyu ndi Bingu basi ,bvuto a malawi kuwombera manja Ziri zonsee.

 5. KOMASO INU MASAPOTA WA MCP, MWAUZE WA MCP ANATIBELA M’BOMA ZAKA 31, NDALAMA ZA NKHANI NKHANI PALIBE WOWATSUTSA. KUTILANDA NDALAMA MUNJILA YA MA CARD, KUTILANDA NG’OMBE, MBUZI, NKHUKU, MPAKA MAZILA AKUTI MUNJILA YA MPHATSO ZOKAKAMIZA ABWEZE.

  1. Adyavali mwayiwala kuti mazirawo mumkadya ndinu nomwe agogo anu akatolera? I think it would make sense if you could give your comment according to the story above.

  2. ANTHU AMAGWILA NTCHITO YA YOUTH OSATI KUFUNA AI NDATI MCP IMAKAKAMIZA CHINA CHILICHOSE UKAKANA NDINDENDETU KOMASO OSALILEMBA DZINA LAINE MWA UCHITSILU AI, SO STUPID INE NDINABADWA 1968 ZA MCP KWAINE SI HISTORY ZAMBILI ZOONA NDIMASO WANGA. TINACHOTSA CHIPANI CHA MCP NGATI TIKUCHOTSA CHIPANI CHA ZUNGU. BOLASO AZUNGU ANALI BWINO. BAMBO WANGA MAINE ANABADWA 1918. MAYI WANGA 1928. KOMA BAMBO WANGA SANAGWILEPO ZA U YOUTH, MAIWANGA SANAPANGEPO ZA U YOUTH NGAKHALE KUKAMUVINILA KAMUNZU MPAKA MULUNGU ANAWATENGA.

 6. mai ameneyu akufunika polio wa garu mwina angakhwimwe nzeru ,amalawi onse akufuna kut economy ebwerere mwakale iyeyo ngamaime pachulu kumayankhula kumbuyo kwa garu kut amusiye, 1.7billion si ndalama lochopa ai ,ndekuti mankhwala mu dzipatala ndi ambiri kwabasi , iya akagwere uko ndekuti amai ameneyu ndiyomwe akusogole mbava zonse kumalawi ,kut ziziononga ndalama za misonkho ya amalawi ovutika iwowo kumanjoyo mano ali pamutunda

  1. NGAKHALE MCP INAKHALA IKUTIBELA NDALAMA M’BOMA, KUTILANDA NDALAMA ZA MA CARD OKAKAMIZA. KUTILANDA NG’OMBE, MBUZI, NKHUKU, MPAKA MAZILA KWAWANTHU OSAUKA ZAKA 31, MCP ITIBWEZELE.

 7. Mmmmmmmmm, ndiye mukalowe mmboma inu ooooh akukondeni, mmmhuuu eeeeee, kumaganiza befor tolk, amalawi amva bwanji, mw anachangamuka anasukusula, amapenya kuti mmmmmmm aawooo aii aawooo eeeeee zinena awoozo mmzamisala.

Comments are closed.