Samala ndi mlomo wako, muno simotukwanila Pulezidenti – sipika auza Chakwera

Advertisement
Lazarus Chakwera

Mtsogoleri otsutsa mu nyumba ya malamulo a Lazarus Chakwera dzulo adzudzulidwa ndi Sipika wa nyumba ya malamulo.

A Chakwera adzudzulidwa kamba konyoza Mtsogoleri wa dziko lino a Peter Mutharika kuti iwo ndi kalonga wa mbava ndinso olephela ndi ogunata.

Richard Msowoya
Msowoya: Wadzudzula a Chakwera.

A Chakwera adanena izi lolemba pamene amayankhula mu nyumba ya malamulo. Iwo adali kuyankhapo pa zimene a Mutharika adanena potsegulila nyumbayi.

Mu kuyankha kwawo, a Chakwera adakwelela Paphiri a Mutharika ndi kuwathila nkhoko.

“A Mutharika dziko likuwavuta, iwo ndi olephela ndinso ogunata,” anatelo a Chakwera.

Iwo adanenanso: “a Mutharika ndi kalonga wa mbava amene akutsogolera uchigawenga mu dziko muno, kulibela dziko la Malawi mwa psipsiti.”

Atanena izi a Chakwera, nduna ya achinyamata ndi masewelo a Henry Mussa anaima ndi kupempha a Sipika kuti adzudzule a Chakwera kamba konyoza Mtsogoleri wa dziko.

Sipika adanena kuti afufuze bwino pa nkhaniyo ndipo azapeleka chigamulo.

 Popeleka chigamulo chake lachisanu, Sipika adanena kuti a Chakwera adalakwitsa ndithu poyankhula udyo za Mtsogoleri wa dziko.