Nkasa ndi Bushiri aimba nyimbo imodzi: yotamanda DPP ndi a Mutharika

Advertisement
Shepherd Bushiri

Amwela chikho chimodzi tsopano pa uwiri wawo, oyimba Phungu Joseph Nkasa ndi munthu wa Mulungu Shepherd Bushiri.

Pamene oyimba Joseph Nkasa watulutsa nyimbo yotonza chipani chotsutsa cha Kongeresi uku akutamandila chipani cholamula cha DPP, naye munthu wa Mulungu Bushiri watsimikiza kuti iye padakali pano ndi nganganga pambuyo pa a Mutharika ndi DPP.

 

Joseph Nkasa

A Nkasa atulutsa nyimbo yawo imene mwa zina akudzudzula chipani cha Kongeresi kuti ndi cha nkhanza zothelatu.

A Nkasa amene anena kuti chipani cha Kongeresi chitha kufanizidwa ndi zinthu zopopa magazi, anena kuti chipani cha DPP motsogoleledwa ndi a Peter Mutharika ndicho chapeleka ufulu kwa a Malawi.

Iyi ndi nyimbo yachiwiri yomwe a Nkasa atulutsa ulendo uno yoyamikila DPP, poyamba anayimba ina yonena kuti a Mutharika ndi Yoswa.

Ku mbali inayi, abusa a Bushiri amene amaziti ndi mneneri alengeza kuti iwo akukondwa ndi utsogoleri wa a Peter Mutharika.

“Chisankho chitachitika lero, ine voti yanga ndipatsa Bambo Peter Mutharika ndi chipani chawo cha DPP,” anatelo a Bushiri.

Iwo anati a Mutharika ayesetsa kuchita zazikulu ku mbali yawo pofuna kutukula dziko la Malawi ngakhale kuti mavuto alipo mwina ndi mwina.

A Bushiri anatsindika kuti chitukuko cha miseu chimene a Mutharika alimbikitsa ndicho chawagwila mtima.

Ngakhale zili motele, a Bushiri anatsindika kuti Magetsi ndiwo ali vuto ku Malawi kuno.

Iwo anazipopa kuti atha kuthana ndi vutoli mu masiku awiri zimene anthu akayika kuti ndi zotheka.