Bubgwe la Transporters Association of Malawi (TAM) ladandaula kuti makampani akunja ndiamene akugwiritsidwa ntchito kubweretsa mafuta m’dziko muno kusiya a ku malawi konkuno.
Woyankhulira bungwe la TAM, Frank Banda, wati pano galimoto zakuno zikumatha kutha miyezi inayi kungopatsidwa ntchito kamodzi kokha.
Banda amayankhula izi kudzera mu pulogalamu ina ndi imodzi mwa nyumba yowulutsa mawu m’dziko muno.
Iye wati kuyambila mu chaka cha 2016 ndi nthawi yomwe ndondomeko ya kanyamulidwe kamafuta kanasokonekela chifukwa cha anthu ena oganiza mwa okha amene anakhazikitsa njira yokuti kampani imene akuyigula mafuta kunja isizankha yokha kamapani imene inyamule mafutawo.

“Mmbuyo monsemu timagwiritsa ntchito njira ya ex-tank, imene boma limati likagula mafuta kaya ku Beira port limasankha lokha transpoter kuti apite akatenge mafuta aja abweretse,” adatero Banda.
Banda wati chifukwa kampani zomwe boma limagula mafuta ndi za dziko la Tanzania, ndikovuta kuti asankhe ma kampani a ku Malawi kuti akatenge mafutawo.
Iye wati ma kampani akunjawa analanda ntchito a Malawi, ndipo pachifukwa chimenechi anayesetsa kukambilana ndi boma la DPP mu chaka cha 2017 komanso 2020 koma sizinaphule kanthu.
Banda wati kuyambira nchaka cha 2020 anayesetsa njira zonse kukambilana ndi boma la MCP kuti athane ndi nkhanizi koma mpaka anatuluka m’boma zisanakonzedwe.
Ndipo wati akuyesetsa kukambilana ndi boma za vutoli chifukwa ndi zonvetsa chisoni kuti ndondomeko yonse yokhudza kagulidwe komanso kabweredwe ka mafuta kakhale mmanja mwa anthu obwera.







