Malamulo a pamseu aja ayamba kuluma: wa minibus amulipilitsa K180,000 chifukwa chonyamula ma 4 – 4

281

Ukali wa malamulo a pamseu amene aopseza oyendetsa minibus wayamba kuoneka.

MINIBUSES

Malamulo a pamseu ayamba kuluma

Bwalo la Milandu mu boma la Mulanje lalamula dalayiva wina wa minibus kuti alipile chindapusa cha K180,000 kapena akagwile ukaidi wa kalavula gaga kwa miyezi isanu ndi inayi.

Malinga ndi malipoti, bwaloli lapeza Bambo Ellias James olakwa pa mlandu oika moyo wa anthu pa chiopsezo atawapakila ngati nsomba mu minibus.

Apolisi ati Bambo James anaimitsidwa pa Mkando mu boma la Mulanje ndi mlandu oti anapakila anthu ambiri zomwe zinali kuika moyo wa anthuwo pa chiopsezo.

Iwo ati anawauza Bambo James kuti ulendo wathela pomwepo ndipo iwo anjatidwa. Koma atamva izi Bambo James anayamba kuchita mavuvu.

Apolisi ati pakuchita mavuvu paja, a James anang’amba yunifomu ya wa Polisi ndi kuwathotholela ena awiri zizindikiro pa zisoti zawo. Komabe Apolisi anawagonjetsa ndi kuwathila unyolo.

Atapita nawo pa bwalo, a Khoti anawapeza olakwa pa mlandu oika miyoyo ya anthu pa chiopsezo ndi okana kumangidwa.

Pa mlandu oika anthu pa chiopsezo kamba kopakila ma folo folo, Bambo James analamulidwa kupeleka K150, 000 ndipo pa mlandu okana kumangidwa, analamulidwa kupeleka K30, 000.

A bwalo anaonjezelapo kuti akalephela kupeleka, akatsekeledwe kwa miyezi isanu ndi inayi.

Share.
  • Opinion