Tony Chitsulo alowa mmanda

Advertisement
Tony Chitsulo burial

A Malawi ochuluka zedi anasonkhana ku Bangwe mu mzinda wa Blantyre loweruka kukapereka ulemu wawo omaliza kwa osewera mpira wakale wa timu ya Bangwe Madrid, Silver Strikers, BeForward Wanderers ndi timu yachisodzela ya dziko lino  Tony Chitsulo amene anamwalira lachisanu madzulo ali ndi zaka 32.

Chitsulo anatisiya pa chipatala cha Queen Elizabeth Central, ku Blantyre atavutika ndi nthenda ya chifukwa chachikulu cha TB.

Tony Chitsulo burial
Thupi la Tony Chitsulo kulowa mmanda.

Akuluakulu oyendesa mpira kuti ku bungwe la  Football Association of Malawi (FAM) adalinso pa mwambowu monga a  Daud Suleiman ndi ena ochokera ku Super League of Malawi (Sulom) akuluakulu, Silver Strikers ndi Nyasa Big Bullets akuluakulu ndi okonda mpira.

Mu mawu ake, Suleiman anati imfa Chitsulo ndi yomvesa chisoni zedi kamba koti adali osewera waluso komanso wamphamvu kwambiri.

“Tony anali mwala wa mtengo wapatali wa m’masiku ake pamene ankasewera ndi timu ya Flames yayingo’no ndi Silver Strikers. Imfa yake yafika pa nthawi imene ife tinkaganiza zokweza masewerowa mdziko muno pogwira nthchito ndi akatswiri ngati iyeyu. Ife kwathu ndikudandaula ndipo Tony timusowa kwambiri” anatero a Suleiman.

Chitsulo adatchuka mu 2008 pamene  anali mu timu yaying’ono ya Malawi mu Under  17 ku Zone Six Championship komanso adasewera bwino kwambiri ku Under 17 African Championship Youth mu dziko la Algeria.

Patapita chaka chimodzi, malemu Chitsulo adachita bwinonso kwambiri ku mpikisano wa osewera osapitilira zaka 20 mu dziko lonse lapansi ku Nigeria ndipo sizinali zosadabwisa kuti mphunzitsi wa timu yayikulu ya Malawi a Kinna Phiri mu nthawi imeneyo adamuitana kuti alowe mu timu yayikulu mdziko muno.

Komabe, Chitsulo adadabwisa anthu ambiri pamene adakana kukalowa ku timu yayikuluyi.

Mu 2009, Chitsulo anapambana mphoto ya osewera ogolesa zigoli zambiri mu ligi ndipo iye ndi Green Harawa adali oswera ofunikila komanso mphangala za Silver Strikers.

Ukatswiri wake udazizila pamene adalowa mu mikangano ndi matimu a Wanderers komanso Silver Strikers pamene ankafuna kukayamba kusewera ku Wanderers.

Tony wasiya mwana wa mkazi wa zaka zitatu.