Tony Chitsulo alowa mmanda

Tony Chitsulo burial

A Malawi ochuluka zedi anasonkhana ku Bangwe mu mzinda wa Blantyre loweruka kukapereka ulemu wawo omaliza kwa osewera mpira wakale wa timu ya Bangwe Madrid, Silver Strikers, BeForward Wanderers ndi timu yachisodzela ya dziko lino  Tony Chitsulo amene anamwalira lachisanu madzulo ali ndi zaka 32.

Chitsulo anatisiya pa chipatala cha Queen Elizabeth Central, ku Blantyre atavutika ndi nthenda ya chifukwa chachikulu cha TB.

Tony Chitsulo burial
Thupi la Tony Chitsulo kulowa mmanda.

Akuluakulu oyendesa mpira kuti ku bungwe la  Football Association of Malawi (FAM) adalinso pa mwambowu monga a  Daud Suleiman ndi ena ochokera ku Super League of Malawi (Sulom) akuluakulu, Silver Strikers ndi Nyasa Big Bullets akuluakulu ndi okonda mpira.

Mu mawu ake, Suleiman anati imfa Chitsulo ndi yomvesa chisoni zedi kamba koti adali osewera waluso komanso wamphamvu kwambiri.

“Tony anali mwala wa mtengo wapatali wa m’masiku ake pamene ankasewera ndi timu ya Flames yayingo’no ndi Silver Strikers. Imfa yake yafika pa nthawi imene ife tinkaganiza zokweza masewerowa mdziko muno pogwira nthchito ndi akatswiri ngati iyeyu. Ife kwathu ndikudandaula ndipo Tony timusowa kwambiri” anatero a Suleiman.

Chitsulo adatchuka mu 2008 pamene  anali mu timu yaying’ono ya Malawi mu Under  17 ku Zone Six Championship komanso adasewera bwino kwambiri ku Under 17 African Championship Youth mu dziko la Algeria.

Patapita chaka chimodzi, malemu Chitsulo adachita bwinonso kwambiri ku mpikisano wa osewera osapitilira zaka 20 mu dziko lonse lapansi ku Nigeria ndipo sizinali zosadabwisa kuti mphunzitsi wa timu yayikulu ya Malawi a Kinna Phiri mu nthawi imeneyo adamuitana kuti alowe mu timu yayikulu mdziko muno.

Komabe, Chitsulo adadabwisa anthu ambiri pamene adakana kukalowa ku timu yayikuluyi.

Mu 2009, Chitsulo anapambana mphoto ya osewera ogolesa zigoli zambiri mu ligi ndipo iye ndi Green Harawa adali oswera ofunikila komanso mphangala za Silver Strikers.

Ukatswiri wake udazizila pamene adalowa mu mikangano ndi matimu a Wanderers komanso Silver Strikers pamene ankafuna kukayamba kusewera ku Wanderers.

Tony wasiya mwana wa mkazi wa zaka zitatu.

Advertisement

256 Comments

 1. Aàaa mutimakuwawa lusulathu Lilibephindu amalawi kodi izizoona wosewela mpila mumatimu akulu akulu kupita ngatiumo kodi amalawi ndalamazanuzo inumuzapitanazo,???? aaaaaaaaaa,aaaaaaa, amalawizachisoni

 2. Aàaa mutimakuwawa lusulathu Lilibephindu amalawi kodi izizoona wosewela mpila mumatimu akulu akulu kupita ngatiumo kodi amalawi ndalamazanuzo inumuzapitanazo,???? aaaaaaaaaa,aaaaaaa, amalawizachisoni

 3. R .I. P Tony Chitsulo, the product of Bangwe Madrid,we will miss u brother man.

 4. Football association of Malawi and to all the teams chitsilo has played for, you can’t even manage to buy a nice coffin for this young lad shame to you guys koma kumangonyopola makobidi football ln malawi will never succeeded shamee

 5. A silver muthu ity anakuthandizani kutenga cup koma opanda player modzi olo chopereka Somali zovesa chisoni ,tithokoze peter wadabwa popelekezaa zake ndi jelesi lufeyo inosi chatama koma Somali zovesa chisoni chifukwa kunalibe olo modzi ochokera ky fam ill silver

 6. Plc guyz don,t just crying about coffin we must know to say is nothing,Is batter we must crying about he life guyz.chofunika kumulila aname angawa nikunganiza zaiwe nine izi zapita next time is u and me.We must know this your sins can be washed a way through the atonement jesus accomprished by shedding his blood on the cross, even if you think you are the worst person in the world, You can turn to jesus for comprete forgiveness.You can pray jesus i believe you,re and savior.Ibelieve that you died on the cross and lose again so that i can have new life in you.I askd to wash away my sins through your creansing blood and make me crean.Fill me with hory spirit so that i can live for you.commit my live to you aman.

 7. Ku malawi umphawi ulikodi! Player bokosi limenelo???? Mwapangitsa manyazi bolani simukadawonetsa pa Fb yapa. Ngati chuma chidavuta bwanji simudatipenphe kuno ku Mozambique tikadagula coffin labwino labwino, osati limenelo ai.

 8. Ku malawi umphawi ulikodi! Player bokosi limenelo???? Mwapangitsa manyazi bolani simukadawonetsa pa Fb yapa. Ngati chuma chidavuta bwanji simudatipenphe kuno ku Mozambique tikadagula coffin labwino labwino, osati limenelo ai.

 9. Patsiku lomari abale anga ndilowoophya tisamare za ulendowu udzifuse wekhaNDIDZATANI?NDIDZAYANKHANJI? NDIKAFIKIRA KUTTI?

 10. Ngakhale ine mzapite mumphasa koma iyayi abale zaenjeza,pamatenda kaya maliro onse okhuzidwa tisamakondere tiyeni tizithandizana.

 11. Ngakhale ine mzapite mumphasa koma iyayi abale zaenjeza,pamatenda kaya maliro onse okhuzidwa tisamakondere tiyeni tizithandizana.

 12. Koma yaaa bokosi choncho ngati mukuika wakuba,,, ntchito anagwira mwana uyuyu?
  Nde kumazabwera ndi nzeru zommangira chiliza chapamwamba atakhala m’bale wanga mpaka ntakusakani ndi chikwanje ndithu inu a FAM,silver ndi noma mmmmm zokhuza kobasi!!
  Rest in peace!!

 13. Koma yaaa bokosi choncho ngati mukuika wakuba,,, ntchito anagwira mwana uyuyu?
  Nde kumazabwera ndi nzeru zommangira chiliza chapamwamba atakhala m’bale wanga mpaka ntakusakani ndi chikwanje ndithu inu a FAM,silver ndi noma mmmmm zokhuza kobasi!!
  Rest in peace!!

 14. Okay Koma anthu ndithudi anthu mumaziwa kulankhula, kuteloku inu mumadikila kuti amwalilre nde muzaone Bokosi? Guyz tiyeni tenene zoona pano ndimaona ngati kukanakhala kwabwino Kumuthandiza munthu akadali ndimoyo, apo ndipamene chikondi chimaonekela, tonse tikudziwa ngati dziko tataya munthu amene anali ndiluso lake, koma zoona Amalawi tizikamba zabokosi kuti ndilotani munthu walephela kuthandizidwa Ali ndi moyo mukuganiza ngati olo akadapezeka ogula bokosi londulalo zikadapindula chani? Apa chikondi chidasowa munthu yu adakali ndi Moyo timamva ndithu akubanja akupempha thandizo kwa anthu akufuna kwa bwino osatinso kwa Ma team okha amene Tonny anamenyako mpila ayi, tiyeni tonse tigwidwe manyazi ndi zinthu zochitisa manyazi zimenezi kwa Munthu amene adabadwa nkumakula ndiumunthu nkhani yaikulu ndiyakuti Tonny sitizamuonso mmoyo uno ngati nkotheka kuti kuli kuonananso ndiye ndi Moyo wina yo koma zandikhudza ndipo zitikhudze mzimu wa Tonny Uwunse muntendele

 15. Okay Koma anthu ndithudi anthu mumaziwa kulankhula, kuteloku inu mumadikila kuti amwalilre nde muzaone Bokosi? Guyz tiyeni tenene zoona pano ndimaona ngati kukanakhala kwabwino Kumuthandiza munthu akadali ndimoyo, apo ndipamene chikondi chimaonekela, tonse tikudziwa ngati dziko tataya munthu amene anali ndiluso lake, koma zoona Amalawi tizikamba zabokosi kuti ndilotani munthu walephela kuthandizidwa Ali ndi moyo mukuganiza ngati olo akadapezeka ogula bokosi londulalo zikadapindula chani? Apa chikondi chidasowa munthu yu adakali ndi Moyo timamva ndithu akubanja akupempha thandizo kwa anthu akufuna kwa bwino osatinso kwa Ma team okha amene Tonny anamenyako mpila ayi, tiyeni tonse tigwidwe manyazi ndi zinthu zochitisa manyazi zimenezi kwa Munthu amene adabadwa nkumakula ndiumunthu nkhani yaikulu ndiyakuti Tonny sitizamuonso mmoyo uno ngati nkotheka kuti kuli kuonananso ndiye ndi Moyo wina yo koma zandikhudza ndipo zitikhudze mzimu wa Tonny Uwunse muntendele

 16. Imfa ya Tonny ukhale ulaliki kwa ife otsala, mulungu saona kuti udali ndani, kapena ndiwe ndani, wadyelera kapena sunadyere koma nthawi yako ikakwana yakwana basi. Tonny mulungu akhululuke zochimwa zako

 17. Imfa ya Tonny ukhale ulaliki kwa ife otsala, mulungu saona kuti udali ndani, kapena ndiwe ndani, wadyelera kapena sunadyere koma nthawi yako ikakwana yakwana basi. Tonny mulungu akhululuke zochimwa zako

 18. Ichi chibokosi chikaola. Kodi bwanji mukulira bokosi, mufuna kuwundira chuma mdothi? Chanzeru yapa nkusonkhetsa ndalamazo kuthandiza anthu amoyo ngati ana ake or mkaziwake kapena omake. Bokosi ndi mtembowo zonse zisanduka dothi mwezi wamawa.

  1. Iwe Mwayi Mambosasa III ndife chitsiru komaso mbuli yamunthu. Kulemekeza mtembo ndiye chani? Wakufa sadziwa chili chose koma moyo uwawa amoyo monga ngati ana, mkazi ndi achibale ake. Don’t do things for the people or just a show off buying an expensive casket just 4 people to see. Kkkkkkk! Kulemekeza mtembo ndiye chani masiku ovuta chuma ngati ano? Pathako pako!

 19. Ichi chibokosi chikaola. Kodi bwanji mukulira bokosi, mufuna kuwundira chuma mdothi? Chanzeru yapa nkusonkhetsa ndalamazo kuthandiza anthu amoyo ngati ana ake or mkaziwake kapena omake. Bokosi ndi mtembowo zonse zisanduka dothi mwezi wamawa.

  1. Iwe Mwayi Mambosasa III ndife chitsiru komaso mbuli yamunthu. Kulemekeza mtembo ndiye chani? Wakufa sadziwa chili chose koma moyo uwawa amoyo monga ngati ana, mkazi ndi achibale ake. Don’t do things for the people or just a show off buying an expensive casket just 4 people to see. Kkkkkkk! Kulemekeza mtembo ndiye chani masiku ovuta chuma ngati ano? Pathako pako!

 20. Ndizoona kuti bokosi lilibe ntchito coz of zipembezo koma Tony anayenera kuikidwa mwa ulemu pa ntchito yomwe anagwira ku fuko la a Malawi, even likanakhala jeneza linayenera kukhala losiyana ndi lomwe amatengera munthu wamba kusonyeza kusiyana. Apapa zitsiru ndi President wa FAM ndi omusatira ake, ndi ma club womwe wakhala akuwatumikira . FAM President do you mean that you didn’t knew who was Tony ? Ndi uve waukulu mwachita apawu guys kulibwino ndiye muthetse mabungwe amenewo akungowononga ndalama za boma zaulere. And I think it’s better to send uve mwachitawu ku bungwe lalikulu la FIFA Watch out guys

  1. Walter nyamilandu machende ake ndithu…..komanso panya pa malemu agogo ake. Amangodzikundikira Chuma….galu ameneyu. Atumbuka si anthu……monga samamudziwa Tonny? Ntchito kupha azikazi basi, kukhwimira u FAM president.

 21. Ndizoona kuti bokosi lilibe ntchito coz of zipembezo koma Tony anayenera kuikidwa mwa ulemu pa ntchito yomwe anagwira ku fuko la a Malawi, even likanakhala jeneza linayenera kukhala losiyana ndi lomwe amatengera munthu wamba kusonyeza kusiyana. Apapa zitsiru ndi President wa FAM ndi omusatira ake, ndi ma club womwe wakhala akuwatumikira . FAM President do you mean that you didn’t knew who was Tony ? Ndi uve waukulu mwachita apawu guys kulibwino ndiye muthetse mabungwe amenewo akungowononga ndalama za boma zaulere. And I think it’s better to send uve mwachitawu ku bungwe lalikulu la FIFA Watch out guys

  1. Walter nyamilandu machende ake ndithu…..komanso panya pa malemu agogo ake. Amangodzikundikira Chuma….galu ameneyu. Atumbuka si anthu……monga samamudziwa Tonny? Ntchito kupha azikazi basi, kukhwimira u FAM president.

 22. Ine ndikuona kuti Ku farm kapena mmatimu mukhale nthumba lapadera lothandizila ma player amene anasewelapo super. League akamwalila.zabokosizi zandinyasa guys

 23. Ine ndikuona kuti Ku farm kapena mmatimu mukhale nthumba lapadera lothandizila ma player amene anasewelapo super. League akamwalila.zabokosizi zandinyasa guys

 24. MMmm nanu picture wangoika iyo phuma bwanji, u need civic education.imvani uthengawo not picture.shame shame shame,.picture waika malinga ndi uthengawo.hey koma amalawife kuchuluka nzeru zopusa.

 25. Ngat a silver & Manoma talephera kumugulira bokosi labwino kma chiliza chake tidzamanga? Why don’t you follow what the peoples team did to deseced Douglas chilambo shame to you.

 26. Brethren… okufa sadziwa kanthu konse…Tony chitsulo iye wapita…kwa sala inu ndi ine …funso nkumati kodi pakutha pamoyo uno ngati zateremu bale wathuyi,tizakafikila kuti? yesu khristu anawakaniza azimai kumulilira ali muchiphinjo chosenza mtanda…anati musalilire ine koma inu nokha ndi ana anu,(Luka 23:28)…mawu wa munawatanthauzila motani abale anga? tiyeni tikonze moyo wathu kuti pakutha pa zonse tizakafikile pabwino….siyani za Bokosi lake kuti linali Lotani…..simungalemekeze maliro …koma mzimu wake okha ngati wafikila kumpumulo….zikomo…Ambuye akudalitseni nonse

 27. Brethren… okufa sadziwa kanthu konse…Tony chitsulo iye wapita…kwa sala inu ndi ine …funso nkumati kodi pakutha pamoyo uno ngati zateremu bale wathuyi,tizakafikila kuti? yesu khristu anawakaniza azimai kumulilira ali muchiphinjo chosenza mtanda…anati musalilire ine koma inu nokha ndi ana anu,(Luka 23:28)…mawu wa munawatanthauzila motani abale anga? tiyeni tikonze moyo wathu kuti pakutha pa zonse tizakafikile pabwino….siyani za Bokosi lake kuti linali Lotani…..simungalemekeze maliro …koma mzimu wake okha ngati wafikila kumpumulo….zikomo…Ambuye akudalitseni nonse

 28. Kodi anthu inu kumaliro mumapitira zifukwa eti simudziwa kuti infa ndi infa basi,komanso ndiyopweteka Kwa aliyense kaya olemera osauka chimodzi ngati sukugwira ntchito yomusangalasa mulungu palibe chako ndiye even bokosi lako litakhala lodula,ndimaona ngati tonse tidandaula kuti munthuyu amafunika maliro ake aendesedwe ndi asilikali state funeral mesa adasewelerako dziko.

 29. A FAM Silver Wanderers Masupporter kodi tinakasonkha limodzilimodzi zizikanakwana ndalama zogula bokosi labwino . Kupita choncho ngati sanamenye mpila . Ndizovetsa chisoni kwambili. Tiyeni tidziwalemekeza aluso athu

  1. Ndizowonadi vuto la ma club ndi limeneli amasangalala pamene player akusewela mpila koma zikamugwela basi ubale wathapo zomvesa chisoni RIP.

  2. Kufa ndikufa koma ifa zina ndizoti zingathe kutetezedwa . Mmene zaonekelamu apa ndizakuti olo nthawi imene amadwala mwinaso thandizo labwino amalisowa chonsecho timakupiza mascaff kunyadila akachinya chigoli .chikondi chankwangwa tisiye

  3. Ngati anthu amafuna kuthandiza ndibwino kumuthabdixa munthu ali moyo it doesn’t make sense kumugulila bokosi londula yet alimoyo amasowa even 500kwacha

  4. What matters most is the legacy he has left behind…we all know Malawi football, players welfare is just a Mockery.if there is anything that has to be done now,is to support his family,otherwise crying over an expensive coffin ,its too little too late

 30. A FAM Silver Wanderers Masupporter kodi tinakasonkha limodzilimodzi zizikanakwana ndalama zogula bokosi labwino . Kupita choncho ngati sanamenye mpila . Ndizovetsa chisoni kwambili. Tiyeni tidziwalemekeza aluso athu

  1. Ndizowonadi vuto la ma club ndi limeneli amasangalala pamene player akusewela mpila koma zikamugwela basi ubale wathapo zomvesa chisoni RIP.

  2. Kufa ndikufa koma ifa zina ndizoti zingathe kutetezedwa . Mmene zaonekelamu apa ndizakuti olo nthawi imene amadwala mwinaso thandizo labwino amalisowa chonsecho timakupiza mascaff kunyadila akachinya chigoli .chikondi chankwangwa tisiye

  3. Ngati anthu amafuna kuthandiza ndibwino kumuthabdixa munthu ali moyo it doesn’t make sense kumugulila bokosi londula yet alimoyo amasowa even 500kwacha

  4. What matters most is the legacy he has left behind…we all know Malawi football, players welfare is just a Mockery.if there is anything that has to be done now,is to support his family,otherwise crying over an expensive coffin ,its too little too late

 31. Please kwa ma team onse tiyeni tiziwasamalira ma player athu osamangowakonda kamba ka ntchito zawo ai komanso kumawathandiza zikavuta.

 32. Please kwa ma team onse tiyeni tiziwasamalira ma player athu osamangowakonda kamba ka ntchito zawo ai komanso kumawathandiza zikavuta.

 33. Mwana waluso. Mmodzi mwa ana anakamenya youth world cup. Former topgoal scorer mu league. But lack of player management kuno kwathu .Noma/silver imati ndi wawo.kutha kwa luso kunali komweko. Sad

  1. Both teams exploited the guy. He had to live more than a season without mpila and not knowing who was to pay his salary. Even during his sickness, none of the teams showed remorse. Kuno ku malawi tilibe ma player agent/manager. So club will use u and leave

  2. I question your reasoning skills? what happened when was playing for silver strikers? Tell me he wasn’t getting paid! Who come in and worsen the situation to this extent?????

 34. Mwana waluso. Mmodzi mwa ana anakamenya youth world cup. Former topgoal scorer mu league. But lack of player management kuno kwathu .Noma/silver imati ndi wawo.kutha kwa luso kunali komweko. Sad

  1. Both teams exploited the guy. He had to live more than a season without mpila and not knowing who was to pay his salary. Even during his sickness, none of the teams showed remorse. Kuno ku malawi tilibe ma player agent/manager. So club will use u and leave

  2. I question your reasoning skills? what happened when was playing for silver strikers? Tell me he wasn’t getting paid! Who come in and worsen the situation to this extent?????

 35. uyo lake lapita lasala la iwe ndiine m bale,kodi udzayankha chani kwamwini moyo poganizira zintchito zako zija?

 36. uyo lake lapita lasala la iwe ndiine m bale,kodi udzayankha chani kwamwini moyo poganizira zintchito zako zija?

 37. Bokosi lokha limasonyeza kuti munthuyu analidi oyimila dziko koma kupita m’bokosi ngati munthu wanba?????Amalawi phunzilani kubwezela ulemu omwe ana anufe timapeleka choooonde…

  1. Malilowa añayenela kuyendesedwa ndi state(state funeral) coz amagwira ntchito ya boma mwanayu just imagine flames under 20 what so ever ndi boma limenelo .So look how he is gone??Very shame Malawi

  2. Komanso how sure are we kuti ilidi ndi bokosi lomwe Tonny waikidwa. A media more especially a online, amatha kungotenga chithunzi cha kwina kwake bola nkhani akufuna kulembayo ikufanana ndi chithunzicho. Rip Wiltord

  3. KAYA BOKOSI NLOTCHIPA KAYA NLODULA KOMA INFA NJOWAWA BASI NDIPO PALIBE KUSINTHA KAYA ZANU IZO BOLA INE NZAKULUNGIDWA MUNSALU YOYERA SANDA

 38. Bokosi lokha limasonyeza kuti munthuyu analidi oyimila dziko koma kupita m’bokosi ngati munthu wanba?????Amalawi phunzilani kubwezela ulemu omwe ana anufe timapeleka choooonde…

  1. Malilowa añayenela kuyendesedwa ndi state(state funeral) coz amagwira ntchito ya boma mwanayu just imagine flames under 20 what so ever ndi boma limenelo .So look how he is gone??Very shame Malawi

  2. Komanso how sure are we kuti ilidi ndi bokosi lomwe Tonny waikidwa. A media more especially a online, amatha kungotenga chithunzi cha kwina kwake bola nkhani akufuna kulembayo ikufanana ndi chithunzicho. Rip Wiltord

  3. KAYA BOKOSI NLOTCHIPA KAYA NLODULA KOMA INFA NJOWAWA BASI NDIPO PALIBE KUSINTHA KAYA ZANU IZO BOLA INE NZAKULUNGIDWA MUNSALU YOYERA SANDA

  1. By bro, we came with nothing and we will go with nothing..what will expensive coffin will help a person on judgment day? Only good deeds will matter on that day.

  2. This guy has a very good point. Munthu wasewera Noma,silver and flames. Angaikidwe mu bokosi lotchipa ngati limenero? Shame malawians tili ndi moyo omangogwirisana ntchito ngat ngolo. Mximu wako uuse muntendere bra. We no you are somewhere on a safe place

  3. Koditu wathu akuona nditchito yomwe amagwira aaaaa amalawi tiyeni tikondane. poti muthu amene wagonayo ndiotchuka ngati udindo wa upresedint oyang’anira dziko or even boma limayenera kuchita kathupo kugoti malawi salibwino basi nde nzose kugoti nzikhare zanu basi!!! Amalawi tatani koditu.

Comments are closed.