Mayi Hellen Singh amwalira

Advertisement
Hellen Singh

Mmodzi mwa yemwe adapikisana nawo pa mpando wa utsogoleri m’dziko la Malawi pa zisankho za m’chaka cha 2014 mayi busa Hellen Singh amwalira usiku wa loweluka.

Hellen Singh
Hellen Singh atisiya.

Mayi Singh omwe anali mtsogoleri wa chipani cha United Independence Party (UIP) amwalira ku chipatala cha Adventist ku Blantyre atadwala kwa nthawi yayitali malingana ndi maripoti omwe Malawi24 yapeza.

Iwo adali m’modzi mwa azimayi awiri mwa atsogoleri onse khumi ndi awiri omwe adapikisana nawo mu chisankho cha patatu choyamba patadutsa nthawi yayitali mchaka cha 2014.

Mayi wa adalinso mwini wa kampani yobwerekesa magalimoto ya SS.

Zambiri tikupatsirani mu maripoti athu osatila.