Kalindo watuluka pa belo

Advertisement
Winiko

Bwalo la milandu munzinda wa Lilongwe lapereka belo kwa Bon Kalindo yemwe anamangidwa pomuganizira kuti anafalitsa uthenga omwe unali ndikuthekera kobweretsa chisokonezo okhudza ngozi ya ndege yomwe inapha wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino a Saulos Chilima ndi anthu asanu ndi atatu.

Lachiwiri pa 25 June 2024, Kalindo anakaonekera ku bwalo la milandu komwe wakana mlandu omwe akuzengedwa oyankhula zinthu zomwe zingadzetse chisokonezo m’dziko.

Potsatira izi, Principal Resident Magistrate Roderick Michongwe wapeleka belo kwa Kalindo yemwe anamangidwa kamba ka kilipi yomwe anatulutsa sabata yatha momwe amakamba za ngozi ya ndege.

Mwa zina, Michongwe wapeleka belo kwa Kalindo pa mfundo zoti omenyera ufuluyu apeleke chikole, asapangeso chili chose chosokoneza mtendere m’dziko muno komaso adzikaonekera ku bwalo la milandu pa masiku oyikika.

Kalindo anamangidwa tsiku limodzi ndi phungu wa nyumba ya malamulo m’dera la ku m’mawa kwa boma la Rumphi a Kamlepo Kalua pa milandu yofanana yomwe ndikufalitsa uthenga wabodza kudzera pa makina a intaneti zomwe akuti zinali ndikuthekera kosokoneza bata m’dziko.

Lolemba sabata ino, apolisi amangaso m’busa Kondwani Chimbirima Gondwe wa mpingo wa CCAP ku Zolozolo munzinda wa Mzuzu pa mlandu ofanana ndi womwe a Kalindo komaso a Kalua akuganizilidwa.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.