Chilima ndi nthochi yosapsa – watelo Ben Phiri

Advertisement
Saulos Chilima

Pamene moto umene anayatsa alamu a mtsogoleri wa dziko lino Mayi Callista Mutharika ukukhala ngati ukuvuta kuthimitsa, amene ali ndi udindo wa zothamangathamanga mu chipani cholamula a Ben Phiri ati kunena kuti Chilima atenge utsogoleri wa chipanichi ndi kulakwitsa.

A Phiri amene nawo anenedwa kuti akuzembelera utsogoleri wa chipani cholumulachi ati padakali pano a Chilima sanapse ndi kufika poti angatsogolere chipani cha DPP.

Saulos Chilima
Phiri: a Chilima sanapse.

Polankhula pa msonkhano wa atolankhani umene iwo anachititsa mu mzinda wa Lilongwe, a Phiri anati a Chilima akuyenela kaye kupitiliza kuphunzila ndale pansi pa a Peter Mutharika zisanakambidwe zoti atenge udindo.

Iwo anafanizila a Chilima ndi ntchochi. Iwo anati nthochi ndi chipatso cha bwino koma munthu akafuna kuidya isanapse, imapeleka khambi.

“Sikuti a Chilima sangakhale mtsogoleri iyayi,” anatelo a Phiri. Ndipo anapitiliza:

“Koma muone, ngati nthochi. Nthochi ndi chipatso chabwino koma ukadya isanapse imakupatsa mavuto angapo ndithu monga kukuchititsa khambi.”

Pa nkhani yoti iwo akuzembelera utsogoleri wa chipani cha DPP, a Phiri anakanika kumasukapo. Iwo anangoti sachita zinthu mwa ngozi koma mwa dongosolo.

Advertisement

3 Comments

  1. Bootlicker…..
    Chilima is :
    A technocrat, and is sellable both in the private and public sector unlike you.

Comments are closed.