Ine ndi MCP mpaka kumanda – Mussa

Advertisement
Uladi Mussa

A Uladi Mussa omwe amatchukanso ndi dzina loti a Chenji golo, anenetsa kuti iwo sadzatuluka mu chipani cha Malawi Congress kamba koti afika tsopano.

A Mussa anena izi pa pulogalamu ya Cruise 5 ya pakanema wa Zodiak.

Potengera khalidwe lawo lomasintha zipani ngati malaya, Joab Frank Chakhaza anawafunsa kuti ndi chifukwa chiyani amangosintha zipani, iwo poyankha ati siadyera ayi.

Iwo anati sadzalowanso zipani zing’onozing’ono ndipo akudziwa kuti chipani cha MCP sichigonja pamasankho a chaka chino.

“Ine sindidzatulukanso chipani cha Malawi Congress, ine ndi MCP mpaka kumanda,” atero a Mussa.

Pakulankhula kwawo anapitiliza kunena kuti iwo ndi malemu Bingu Wa Mutharika anali khethekhethe kukondana ndipo pa chilichonse chochitika m’dziko muno a Wa Mutharika amawaitana kuti akambilane nawo.

Pokambapo pa za kuvuta kwa mafuta a galimoto m’dziko muno, a Mussa ati vutoli kuti lithe Malawi akuyenera kupeza njira zina zopezera forex ndipo mavuta ali m’dziko muno anakakhalapo mtsogoleri wina akanakumananso nawo.