Odi ine nditsike! Nyalonje wautaya udindo

Advertisement
Saulos Chilima

Bwato la ulendo wa ku Kenani lakumana ndi mafunde, ndipo ena adindo ayamba kuzitaya.

Nduna yoona za ntchito, mayi Agnes Nyalonje, atula pansi udindo wawo tsopano. Izi zachitika patangodutsa tsiku limodzi zotsatira za kafukufuku zitaonetsa kuti chipani cha Kongeresi chili ndi mwayi ochepa opambana chisankho cha 2025 kusiyana ndi chipani cha DPP.

Koma Mayi Nyalonje ati iwo sakutula pansi chifukwa cha nkhani imeneyo. Iwo ati imfa ya amene adali wachiwiri wa a Chakwera, a Chilima, ndiyo yawapangitsa kutula pansi udindo.

Agnes Nyalonje Robert Ridley
Nyalonje wautaya unduna

Malinga ndi malipoti ena, Mayi Nyalonje ati adadziwitsa mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera khumbo lawo lofuna kuzitaya mu July chaka chino itatha nthawi yolira maliro a Chilima.

Malipotiwo ati a Chakwera adakana kuti Mayi Nyalonje atule pansi udindo poopa kuti zisokoneza m’mene anthu amaonera imfa ya Chilima.

Kuyambira nthawi imeneyo, Mayi Nyalonje akhala asakugwira ntchito yawo ngati nduna kwenikweni. Nthawi zambiri akhala asakuonekera ku zochitika zokhudzana ndi unduna wawo.

Pamene nyumba ya malamulo ili mkati kukumana, mayi Nyalonje akhala osapita ku nyumbayi ndipo sabata latha lomweli a kumbali ya boma anauza nyumbayi kuti mafunso onse opita ku unduna wa Mayi Nyalonje awasunge kaye chifukwa palibe oyankhapo.

Usiku wa pa chiweru, mayi Nyalonje adatsimikiza kuti iwo basi azitaya za boma la mgwirizano la Tonse.

“Imfa ya Chilima idasintha zinthu zambiri basi, sindikanapitiriza,” iwo anatero.