Achinyamata adzikhala ndi mipando ya padera ku nyumba ya Malamulo – Mtumbuka

Advertisement
Matthews Mtumbuka

A Matthews Mtumbuka, omwe alinawo m’gulu lofuna kudzapikisana nawo pa mpando wa utsogoleri kuchipani cha United Transformation (UTM) ati ali ndi malingaliro ofuna kudzayambitsa zoti achinyamata pamodzi ndi amayi azidzakhala ndi mipando yawo yapadera ku nyumba yamalamulo.

Iwo amayankhula izi kusukulu yaukachenjede ya Mzuzu pamwambo wamgonelo omwe sukuluyi idakonza pofuna kupeza ndalama zochitira mwambo wa ophunzira omwe amaliza maphunziro awo.

Iwo adati achinyamata m’dziko muno ndi ochuluka ndipo ndiwopitilira ma peresenti 60 pachiwerengero cha anthu choncho akuyenera kumapatsidwa mwayi pa ntchito zachitukuko.

Pamenepa a Mtumbuka analimbikitsa ophunzirawo kuti adzilimbikira ndipo achepetse mtima wansanje popeza munthu wa nsanje sangapange chitukuko pamoyo wake.

Iwo adawuzanso ophunzirawo kuti adzikhala ndi masomphenya pa moyo wawo chifukwa adati munthu opanda masomphenya sangakhale otukuka pachuma.

“Tiyeni ife achinyamata tisamadzidelere pochita zinthu popoza tsogolo la dziko lino liri m’manja mwathu popeza ndife atsogoleri alero,” anafotokoza motero.

M’mawu ake, wachiwiri kwa mkulu wa sukuluyi ukachenjede ya Mzuzu a Walles Singini adathokoza a Mtumbuka chifukwa chodzakhala nawo pamwambowu omwe udakonzedwa ngati njira imodzi yopezera ndalama.

Advertisement