Nkhonya yobwezera kuwawa: Gabadinho awumbuza Peter Banda

Advertisement

Kudali nkhondo ya angitawo usiku wapitawu mu dziko la South Africa pamene anyamata okankha chikopa mu timu ya dziko lino ya Flames adapindirana ndevu mkamwa mu mpikisano wa CAF Confederations Cup.

Gabadinho Mhango amene amasewera team ya Orlando Pirates ya ku South Africa, adakankhira kwakuya mkubweresa misozi ya chisoni kwa Peter Banda amene amasewera timu ya mu dziko la Tanzania yotchedwa Simba.

Mu masewerowa amene adathera ma penate ndicholinga choti papezeke timu yopitilira mu ndime yachiiwiri kwa yomaliza, Mhango adamwesa chimodzi mwa zigoli kuzela pa penate. Izi zidathandiza Pirates kuti ipambane ndi zigoli zinayi kwa zitatu.

Zisadafike ku ma penate, Pirates idapambana ndi chigoli chimodzi kwa duu. Chigolicho adamwesa ndi Peprah ochokera mu dziko la Ghana.

Izi zidapangisa kuti masewerawo athere wani kwa wani, potengera kuti timu ya Simba idapambananso ndi chigoli chimodzi pa masewera amene adachitikira kwawo ku Tanzania.

Mhango wakhala akumanidwa mpata okwanira osewera mu timu yake kuchokera kumapeto kwa chaka chatha. Masewera a dzulo adachitanso kuchokera panja mu mphindi 77.

Anthu ambiri akuzuzula mphunzitsi wa Pirates Mandla Ncikazi kamba kosapereka mpata okwanira kwa Katswiriyu.