Mpikisano wa Chipiku walowa libolonje


Soccercity Lodges Complaint- Malawi24

Pomwe ena akupanga chotheka kuti mpira udziyendetsedwa mwamakono, ndi pomwe mpikisano wa chigwawo chonse chapakati, wa Chipiku ma timu ena akugwiritsa ntchito kalata yakwa mfumu ngati chinkhoswe mmalo ma khadi ya CRFA.

Malamulo a mpikisanowu amanena kuti osewera akuyenera akuyenera kuvomerezedwa ndi chiphaso cha bungwe lomwe likuyendetsa ndipo osewera akuyenera kukhala mu ndondomeko ya bungwe la FAM, lotchedwa Mpira Connect.

Lamulungu timu ya Ntchisi Select yomwe inakhala akatswiri a m’boma la Ntchisi, imakumana ndi Chimvano Soccer City yaku Ntcheu pa bwalo lazamasewero la Mbabzi ku Lilongwe komwe osewera ena agwiritsidwa ntchito mosemphana ndi malamulo.

Malingana ndi kalata ya dandaulo yomwe wachiwiri kwa mlembi wa Soccer City, a Paul Lemson asainira, ati timu yawo inasewera monyanyala kamba kowuzidwa kuti osewera omwe alibe ma khadi ovomerezeka asewere nawo.

“Tinauzidwa titalowa kale pa bwalo la zamasewero kuti CRFA yaloleza Ntchisi Select kugwiritsa ntchito ma khadi a mzika, kalata zakwa mfumu komaso ena ma khadi akalekale a Division 1 mmalo mwa makhadi ovomerezeka a mpikisanowu” anatero a Lemson.

Iwo afusa CRFA kuti ifufuze nkhaniyi ndikufotokoza bwinobwino malamulo zomwe akukamba komanso ati akufuna bungweli lichitepo kanthu ngati panali kuphwanya malamulo ndicholinga choti chilungamo chiwoneke komaso mbiri ya mpikisanowu isasokonekere.

Mmasewerowa, Ntchisi Select inapambana ndi chigoli chimodzi kwa duuu chomwe chinabwera gawo loyamba.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading