Joe Ikon avulala atadziponya pa siteji


Img 20261025 Wa0019- Malawi24

Mawu woti timba anathyoka mwendo dansi yothaitha aphelezela pa woyimba Joe Ikon yemwe wavulala atichita ukandiyerekere pagulu podziponya pa nsanja.

Woyimbayu anali ndi phwando la mayimbidwe Loweruka munzinda wa Blantyre lomwe amalitcha kuti “Mwana wa Atate” komwe khwimbi linasonkhana.

Kamena wina yemwe akuzungulila pa masamba amchezo, akuonesa Ikon akuchoka pa nsanja ndikudziponya ku malo omwe kunali anthu.

Ngakhale zili choncho, sizikudziwika ngati woyimbayu anavulala podupha kapena ngati wavulala kamba koti anafikira pansi atadumpha.

Pakadali pano, woyimbayu wayika pa tsamba lake la fesibuku chithunzi chowonetsa mwendo omwe wavulala utakutidwa ndi nsalu zakuchipatala.

Komabe, Ikon sanafotokoze kuti wavulala motani koma wangolemba mawu omwe akusonyeza kuti pano akunong’oneza bondo pa zomwe anachitazo.

“Dzulo tinasangalala kwambili khalangati,” walemba choncho Ikon.


.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading