Ng’amba ipitilira m’madera ambiri akumwera – DCCMS


Sun

Pomwe m’madera ambiri a m’chigawo cha ku m’mwera mvula yasiya kugwa, Nthambi yowona Zanyengo mdziko muno ya Department of Climate Change and Meteorological Services (DCCMS) yati nyengo ya ng’amba ipitilirabe m’madera ambiri mchigawo-chi.

Nthambiyi yati maboma amene akhale ndi n’gamba yochuluka ndi Salima ndi Mangochi.

‘Ng’amba ikuyembekezereka kupitilira m’madera ambiri akumwera kuphatikizapo maboma a Salima ndi Mangochi,” yatero DCCMS.

Lero Nthambiyi yati m’madera ambiri makamaka akumpoto ndi pakati akhale ndi nyengo yamitambo komanso ya mvula yamabingu yomwe pena idzigwa yamphamvu.

Masana wa lero m’madera ambiri a mdziko muno ayembekezere nyengo ya mphepo ndi yotentha komanso mvula yamabingu makamaka m’madera a pakati ndi kumpoto pomwe kum’mwera ayembekezere nyengo yamitambo yapatali patali ndi yopanda mvula m’madera ambiri.

DCCMS yati mphepo idziomba kuchokera kumwera chakunvuma koma m’madera omwe mukhale mukugwa mvula idziomba kuchokera mbali zosiyanasiyana ndipo Lachiwiri nyengo ya mvula yamabingu idzapitilira maka m’madera akumpoto ndi pakati.

Latest vacancies

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading