Aphungu adutsitsa bajeti ya mchaka cha 2025/2026

Advertisement

Pomwe nthawi imati 6:30 usiku uno aphungu a kunyumba ya malamulo tsopano adutsitsa ndondomeko ya zachuma ya mchaka cha 2025/2026 yokwana 8.076 trillion Kwacha (K8, 076, 667, 784, 858) yomwe nduna ya zachuma a Simplex Chithyola Banda anapeleka mnyumbayi mwezi watha.

Ndalamazi zapita ku ma unduna ndi ku nthambi za boma ndipo aphungu amadutsitsa imodzi imodzi mpaka onse 62 kuyambira voti 050 mpaka voti 560.

Mtsogoleri wa zokambirana mnyumbayi a Richard Chimwendo Banda ayamika onse kuyambira nduna ya zachuma, aphungu, othandizira sipikala, ma sipikala a mnyumbayi, ndi aMalawi onse pa ntchitoyi.

Iwo ati tsopano aMalawi akhonza kuona okha kuti aphungu awo adzipeleka podutsitsa ndondomeko ya zachumayi.

Itadutsa ndondomeko ya zachumayi aphungu anakhamulira kwa nduna ya zachuma a Simplex Chithyola Banda kuwagwira chanza pa ntchito yomwe agwira yobweletsa ndondomeko ya zachuma yomwe yadutsa opanda ziyangoyango.