
Mgwirizano wa mabungwe oyima paokha m’boma la Balaka ati ndi okhumudwa ndi mpungwepungwe omwe wabuka pakati pa anthu a m’mudzi mwa Ng’onga, khonsolo ya Balaka komanso kampani ya Portland Cement pa nkhani yokhudza chipukuta misonzi cha malo.
Anthu a m’mudzi mwa Ng’onga akudandaula kuti anapatsidwa chipukuta misonzi chochepa poyerekeza ndi kukula kwa malo awo omwe kampani ya Portland Cement inagula ndipo ikumangapo fakitale yopanga Cement.
Sabata yatha, zokambirana zomwe zinalipo pakati pa mbali zonse zokhudzidwa ndi nkhaniyi zinathera mu kusamvana, zomwe zinapangitsa kuti anthu a kwa Ng’onga ayambe kuchita m’bindikiro komanso kutseka zipata zolowera komanso kutulukira ku kampani ya Portland.Izitu akuti zinakhudza kwambiri ntchito za kampaniyi.
Ndipo dzulo lachinayi, apolisi anakhetsa utsi okhetsa misonzi pofuna kubalitsa anthuwa ndipo anthu okwana asanu ndi atatu (8) anamangidwa ndipo akuyembekezeka kukawonekera ku bwalo la milandu komwe akazengedwe milandu.
Komabe, wapampando wa mabungwe oima paokha m’boma la Balaka, Hariex Chimutu, wati ndi okhumudwa kuti adindo akuchedwa kuchitapo kanthu pa nkhaniyi.
“Ndikofunikira kwambiri kuti adindo achitepo kanthu mwansanga madandaulo a anthu a kwa Ng’onga ayankhidwe mwansanga ndipo nditsindike kuti ndi ufulu wawo kuchita ziwonetsero pamene akuwona kuti ufulu wawo ukuphwanyidwa,” anatero a Chimutu.
Lachisanu, nthumwi za mabungwe oima paokha zinakumana ndi mkhalapampando wa khonsolo ya Balaka, Pharaoh Kambiri, wapampando wa komiti yoona za chitukuko ku khonsolo ya Balaka, Osman Mapira, komanso mkulu wa apolisi m’bomali, Dan Sauteni, komwe anakambirana za kofunika kokambirana kuti nkhaniyi ithe mwa bata ndi mtendere.
Pa mkumanowu, mabungwewa anatsindika kuti ndi okonzeka kukumana ndi atsogoleri a nzika zokhudzidwazi kuti akambirane nawo za kufunika kotsata malamulo pamene akupanga ziwonetsero zawo.