A Malawi titseguke m’maso – Makande

Advertisement
DPP Rally

Mkulu okopa anthu mu chipani cha Democratic Progressive (DPP) yemwenso ndi phungu wa nyumba ya malamulo wa dera la pakati cha kum’mawa m’boma la Balaka a Chifundo Makande ati nthawi yakwana tsopano kuti a Malawi atseguke m’maso posankha atsogoleri omwe ali ndi kuthekera kopulumutsa dziko lino ku nsinga za umphawi zomwe zakuta dziko lino.

A Makande anayankhula izi pa sukulu ya Chidalala m’boma la Balaka komwe pamodzi ndi akuluakulu ena a chipanichi anachititsa msonkhano.

“Anthu ambiri m’dziko muno tili pa umphawi wa dzaoneni kaamba kakuti utsogoleri wa chipani cha MCP walephera kuyendetsa dziko lino.

Chifundo Makande
Makande: Umphawi wachuluka.

“Mitengo ya katundu osiyanasiyana yakwera modetsa nkhawa zomwe zapangitsa kuti a Malawi ambiri akhale pa ululu osasimbika,” anatero a Makande.

A Makande omwenso aonetsa chidwi chodzapikisana nawo pa mpando wa phungu wa dera la Balaka Rivirivi amema anthu m’dziko muno kuti adzavotele atsogoleri a chipani cha DPP chifukwa ali ndi masomphenya komanso kuthekera koyendetsa bwino dziko.

Ndipo m’mawu awo, gavanala wa chipani cha DPP m’chigawochi a Daud Chikwanje komanso mkulu wa achinyamata mu chipanichi a Norman Chisale anamema otsatira chipani cha DPP kuti asatengeke ndi andale omwe amalimbikitsa mchitidwe wa ziwawa komanso chisokonezo ndipo m’malo mwake akhale ololera bata komanso umodzi.

Lamulungu, chipani cha DPP chidachititsa misonkhano yoyimayima m’boma la Balaka pofuna kulimbikitsa anthu kuti adzavotele chipanichi mu chisankho cha pa September 16, chaka chino.

Ku msonkhanoku kunalinso akuluakulu ena a chipani cha DPP monga a Victor Musowa, a Shadric Namalomba, a Roza Fatch, a Fyness Mangonjwa ndi ena ambiri.