Chakwera akukanidwa kulikonse

Advertisement
Chakwera

Kuno zipatalazo kulibe, kuno manyumbawo kulibe, kuno ma Mega farm wo kulibe, bodza la Chakwera kuwonekera poyera zamanyazi

Ma khonsolo osiyanasiyana akupitilira kumukana Chakwera monga muja Petro anamukanira Yesu.

Makhonsolowa akukanitsita kwa mtu wagalu kuti zina zomwe anakamba Chakwera mu SONA yake lachisanu lapitali ku nyumba ya malamulo ndi bodza lamkukhuniza.

Khonsolo ya Boma la Machinga lakanitsitsa kuti ku bomalo kulibe minda ikuluikulu (Mega Farms) yomwe Chakwera amati wakhazikitsa.

Nayo khonsolo ya Boma la Mangochi yatsutsa zomwe mkuluyu anakamba ku Nyumba ya malamulo, kuti boma la kongolesi lamanga zipatala zazing’ono za Namayisi ndi Misolo.

Nako ku mzimba khonsolo yakumeneko yati zitukuko zomwe Chakwera amati boma lake lamaliza kupanga kumeneko sizinati mkomwe zina zinakali pa fondeshoni chabe.

Ma khonsolo ena omwe abweletsa bodza la m’tsogoleri wa dzikoyu pambalambanda, pamtetete ndi monga Phalombe, Nsanje, Likoma, Rumphi ndi Chikwawa.

M’tsogoleri wa dziko lino yu, amachita kulakhura mwathamo (ka slang) ku nyumba ya malamulo lachisanu, kuti akutengera a Malawi kutsogolo, ndipo ntchito za manja ake zikumuchitira umboni. Ntchito zina zomwe amenenazo ndi zomwe makhonsolo ambiri azikana kuti ayi ndithu, kuno kulibe zitukuko zimenezo.

Koma mneneri wa chipani cha MCP, Jessie Kabwira, wati ndizotheka kuti zinthu zina zomwe anayankhula mtsogoleri wa dziko lino, Lazarus Chakwera ndi zabodza.

“Ndanena kale, tikamazimitsa moto sitisankha madzi. it’s possible kuti ma figures ena might not be correct, so what?. M’dani wathu ndi DPP, we have an enemy panjira, let’s focus on the enemy. It’s DPP that wants to finish us, it’s not about semantics, let’s focus on that chonde nthawi yatha,” anatero a Kabwira mu kilipi yomwe ikuyenda pa masamba a mchezo.