Mfumu Mwanyanja yaphedwa poiganizira kuti ndi mfiti

Advertisement
Msimwaka

Apolisi m’boma la Chitipa akhazikitsa ntchito yosakasaka amaliwongo osadziwika omwe apha mfumu Mwanyanja, m’dera la mfumu yaikulu Nthalire m’bomalo.

Gladwell Msimwaka, Mneneri wa apolisi ku Chitipa ndiye watsimikiza za nkhaniyi ponena kuti mfumu Mwanyanja, yomwe dzina lake la pa msonkho ndi Mapuzi Kaonga azaka 65, apezeka atafa mu mphepete mwa mseu m’dera lomwe amatsogolera.

Malinga ndi Simwaka, zotsatira zachipatala cha Nthalire zasonyeza kuti mfumuyi yafa chifukwa chotaya magazi kwabwiri kamba ka Mabala amene anali nawo.

Mfumuyi imaganiziridwa kuti ndi mthakati ndipo pa tsiku limene adapezeka itafa, inali ikuchokera ku maliro amene anthu amaganizira kuti mfumuyi ndiye yapha munthuyo kudzera mu ufiti.

Mawu ake Simwaka wachenjeza anthu amene akutengera lamulo m’manja mwawo pomachita za upandu m’dziko muno kuti akagwidwa adzipasidwa chilango chokhwima.