Anjatidwa kamba koba makina akuchipatala

Advertisement
Lilongwe Police

Apolisi anjata bambo wina kaamba koba makina oyezera amayi ku chipatala cha Bwaila mu mzinda wa Lilongwe.

Zadziwika kuti mkuluyuyu dzina lake ndi Justin Makata ndipo ali zaka 27. Malingana ndi mneneri wa Polisi ya Lilongwe, a Hastings Chigalu, mkuluyu amagwira ntchito yothandiza kusamalira odwala (hospital attendant) ku chipatala chi.

“Justin Makata adayamba ntchitoyo chaka chatha, ndipo adachita izi pa 17 January chaka chino. Iye adakagulitsa makinawa pa mtengo wa K2 million koma mtengo wake weniweni ndi K6 million,” atero aChigalu.

A Chigalu ati bamboyu adaulula kuti adakasulitsa makiyi omwe adakatsegulira mu chipinda chomwe mudali makinawo.

Apolisi atachita kafukufuku ndikugwira aMakata, iwo adalondolera a polisi komwe adakagulitsa makinawo.

“Zidadziwika kuti komwe adakagulitsa makinawo ndi kwa mkulu wina yemwe ali ndi chipatala cholipiritsa, ndipo adatengako kale ndalama zokwana K1.8 million, kudatsala K200 000,” anaonjezera aChigalu.

Malingana ndi aChigalu mkuluyu akaonekera ku bwalo la milandu posachedwa komwe akayankhe mulandu wakuba pa malo antchito.

A Makata amachokera m’mudzi wa Makuta, m’boma la Nkhotakota.