ACB yanjata dotolo wa mano ku Lilongwe

Advertisement
KCH

Bungwe lothana ndi ziphuphu ndi katangale la Anti-Corruption Bureau (ACB) lamanga dotolo wa mano pa chipatala cha Kamuzu central mu mzinda wa Lilongwe, chifukwa chokakamiza ovulala pa ngozi kuti apeleke chiphuphu cha K50,000 kusinthana ndi thandizo la ulele la boma.

Malinga ndi yemwe watsina khutu nyumba zina zofalitsa nkhani mdziko muno, dotoloyu yemwe dzina lake ndi Dingiswayo Moyo anakakamiza odwala kuti apeleke 50,000 kuti athe kumuthandiza vuto lake la mano lomwe odwalayu anali nalo.

Odwalayu yemwe anavulala pa ngozi ya njinga za kabhanza anatsina khutu bungwe la ACB pa mkhalidwe okanidwa omwe Dingiswayo Moyo anaonetsa pa chipatala cha boma.

Pakali pano apolisi akusunga a Moyo mu chitolokosi ku polisi ya area 3 mu mzinda omwewu wa Lilongwe komwe akuyembekezera kukayankha milandu yomwe awapatse.

Bungwe la ACB limalimbikitsa aMalawi kuti akaona mchitidwe uliwonse wa chiphuphu ndipo ali ndi umboni okwanila, okhudzidwawa adzipeleka dando lawo ku nthambiyi kuti mchitidwe wa katangale ndi ziphuphu uchepe ndi kutheratu mdziko muno.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.