Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino a Michael Usi alangiza anthu amene akulandira chimanga kudzera mu ndondomeko yothandiza anthu amene akusowa chakudya kuti akalandira chimanga asamale posadya moononga chifukwa ndi chochita kupatsidwa.
A Usi ati kwa olandira chakudyachi adye mwa mlingo oyenera ndipo apempha kwa anthu amene ali ndi chakudya kuti athandize anzawo amene alibe monga mwa chikhalidwe cha chiMalawi.
A Usi atulutsa mawuwa pa mwambo ogawa Chimanga kwa mabanja 961 pa sukulu ya Chikwawa primary m’bomali lachisanu pomwe alangizanso khonsolo ya Chikwawa kuti pogawa chimangachi pasakhale kukondera kulikonse ponena kuti njala siwona malire, chipani, mtundu kapena chipembedzo ndipo chakudya chidzigawidwa mofanana.
Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dzikoyu wati pali andale ena omwe akumaletsa anthu ku madera awo kulandira chimanga pofuna kupeza anthu oti awatsate pemene akuyipitsa ena.
M’modzi mwa adindo ku World Food Programme (WFP) oyimira chigawo cha ku chigwa kwa shire, a Alinafe Kamdonyo ati dongosolo logawa chakudya lipitilira kwa miyezi isanu, ndipo ati afikira kwa anthu pafupifupi 2 million mwa anthu 5.7 omwe anakhudzidwa ndi mavuto odza kamba ka nyengo ya El Niño mdziko muno.
Bwanamkubwa wa boma la Chikwawa a Nadin Kamba ati bomali limakhudzidwa nthawi zonse ndi nkhani zanyengo ndipo ayamika boma ndi bungwe la WFP chifukwa cha thandizoli komanso ma thandizo ena monga mtukula pakhomo.
M’boma la Chikwawa lokha mabanja okwana 85441 omwe ndi anthu pafupifupi 384, 000 akhale akulandira thandizoli.