Mwana wa zaka ziwiri wamwalira m’boma la Mangochi atapsa modetsa nkhawa nyumba yomwe amakhala itayaka moto.
Potsimikiza za ngoziyi, ofalitsa nkhani ku polisi ya Monkey-Bay, Alice Sichali, wati nyumbayi idayaka kamba ka mafuta a galimoto omwe amasungidwa mnyumbayi.
Sichali wati izi zidachitika pa tsiku la khilisimisi pa 25 December, 2025 pa Malo ochitira malonda a Nsaka m’bomali.
Malingana ndi a Sichali, bambo a malemuwa ndi mlovi odziwika bwino m’delari ndipo amasunga mafuta a galimoto mnyumba omwe amagwilitsa ntchito mu ma boti awo a injini.
“Patsikuli, mai a mwanayu komanso mlongo wake anali mnyumba kuphika chakudya pa mbaula.Kenako, malemuwa adayandikira komwe amaphikako atanyamula botolo la mafuta a petrol m’manja zomwe zinapangitsa kuti moto ubuke ndi kufalikira m’nyumba monse,” anafotokoza Sichali.
Zitachitika izi, anthu atatuwa anavulala kwambiri ndipo anathamangira nawo ku chipatala cha Monkey-Bay komwenso adawatumiza kuchipatala chachikulu cha boma la Mangochi komwe malemuwa adamwalira ali mkati molandira thandizo la mankhwala.
Malingana ndi a Sichali, malemuwa amachokera m’mudzi mwa Chimphamba, mfumu yaikulu Nankumba m’bola lomweri la Mangochi.
Pakadalipano, apolisi ku Monkey-Bay achenjeza anthu onse kuti apewe kusunga mafuta a galimoto mnyumba kuti apewe ngozi zonga izi.