
Bishop wa Karonga Diocese, Martin Mtumbuka wawuza mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera kuti mkulu wina wa boma, ananama kuti nseu wa Chiweta-Karonga uli bwino ndipo wati bodza limeneli asaligwiritse ntchito kuchitira kampeni.
Poyankhula pa mwambo odzoza Bishop Yohane Suzgo Nyirenda kukhala bishop wa diocese ya Mzuzu, Bishop Mtumbuka wati munthu wina wamkulu m’boma la a Chakwera anatumiza uthenga oti mseu uli bwino masabata awiri apitawo.
“Ma sabata awiri apitawo munthu wina wamkulu nduganiza kuti ndi wa m’boma lanu anatumiza uthenga kuti nseu wa Chiweta kupita ku Karonga wakonzedwa ndipo kuti palibe mavuto konse”
“Ndufuna ndikupempheni a president musamvere ndi kugwiritsa ntchito uthenga umenewo kuchitira kampeni chifukwa mudzafunsidwa kuti mukunena bodza,” anatero Bishop Mtumbuka
Pa 20 April, nduna ya Boma yowona za mayendedwe ndi zomangamanga, a Jacob Hara anatsutsa kuti zithunzi zina zomwe zikuwonetsa kuyipa kwa nseu wa Chiweta-Karonga nzabodza ndipo nzakale.
A Hara anati zonse zokhudza kukonza ntchito zongoyembekezera m’malo amene ali ovuta mu nseu wa Chiweta- Karonga zinatha ndipo nsewuwu ndi oyendeka pakali pano pomwe akukonza ndondomeko za ntchito yokhazikika.
Bishop Mtumbuka kenako anati pena amagwidwa ndi chisoni kuti amayitana mtsogoleri wa dziko mwakuti mbali inayi amakhalanso akuganizila za kuchepa kwa chuma cha dziko lino chomwe chilipo ndi kuti mtsogoleri wa dziko ayende ku zochitika ngati izi. Apo ndi pomwe anati sangachitile mwina chifukwa kupandanso kuyitana mtsogoleri wa dziko anthu ena amawona ngati pali udani pakati pawo.
Bishop-yu anati pofika pa mlingo umenewu ndi pomwe amagwidwa njakata ndipo amamgoyenera kuyitana mtsogoleri wa dziko.
A Chakwera anakakhala nawo pa mwambo odzoza Bishop Yohane Sugzo Nyirenda yemwe tsopano ndi bishop wa diocese ya Mzuzu.