Silver wa ku CAF, Mponda atiwuze player amene akufuna tigula

Advertisement
Silver Strikers

Gavanala wa Reserve Bank ya Malawi, a Wilson Banda abetchela Peter Mponda ndi osewera ake kuti apanga chilichonse chofunika kuti timuyi isewere mu CAF Champions 2025.

Poyankhula atatha masewelo ndi Premier Bet Dedza Dynamos pa bwalo la Silver ku Lilongwe, naye wachiwiri kwa gavanala wa Bank yi a McDonald Mafuta Mwale wawuza Mponda kuti asake osewera amene akuwafuna, anene zonse zofunika ndipo athandiza zonse ponena kuti Silver yawonetsa kuti ili ndi kuthekera.

“CAF timenya ntchito ikadalipo ndipo tipanga, ndipo timuuze Mponda kuti yamba kuyang’ana osewera omwe ukuwafuna, anenenso zomwe zikufunika ndipo anene chomwe akufuna tipanga,” Mwale anatero.

Akatswiri a ma bankers adzipezera malo ku mpikisano wa CAF omwe ndi wa akatswiri a mu zikho za ma ligi aakulu a mmaiko mwawo iyo itatenga ukatswiri wa TNM Super League kuno ku Malawi.

Silver yatenga ukatswiri wa 2024 TNM Super League itatsiliza masewelo onse 30 kupata ma point 67 ndipo masewelo ake omaliza yapamantha Premier Bet Dedza Dynamos ndi zigoli 5 kwa 2, zigoli kuchokera kwa Chimwemwe Idana , Gift Chunga ziwiri, Duncan Nyoni ndi Zebron Kalima pamene ziwiri za Dedza kuchoka kwa Gift Magola.

Mphunzitsi wa Silver Peter Mponda anati ndi onyadira ndi zomwe anyamata ake awonetsa kuyambira kumayambiliro a ligi kufika pamapeto.

Pamene anyamata a ku area 47 atenga ukatswiri wa TNM, FOMO, Bangwe all stars ndi Baka City atuluka mu ligi ya chaka chino ndipo akayamba tsopano kusewela ma ligi a mzigawo.