Apolisi akupha demokalase – Chaponda

Advertisement
Chaponda

Mtsogoleri wa aphungu otsutsa boma ku Nyumba ya Malamulo a George Chaponda ati zomwe achita apolisi komanso anthu ena omwe alepheletsa ziwonetselo mu nzinda wa Lilongwe ndi m’chitidwe okupha ufulu wa nzika za dziko lino.

A Chaponda anadzuka m’nyumba ya malamulo pamene zokambirana zinayamba ndipo anafunsa sipikala wa nyumbayi a Catherine Gotani Hara ngati zomwe akupanga apolisi ndi zoona mu ulamuliro wa demokalase.

Sipikala Hara anagwirizana ndi funso la a Chaponda koma anauza a Chaponda kuti akuyenera atsate ndondomeko yoyenera kufotokozera nkhaniyo.

Ziwonetselo zomwe linakonza bungwe la Centre for Democracy and Economic Development Initiative (CDEDI) zinathera panjira apolisi limodzi ndi anthu onyamula zikwanje atathamangitsa anthu ochita ziwonetselozi.

Apolisi anafukiza utsi okhetsa misonzi kwa nzikazi zomwe zimachita zionetselo kamba kokwiya ndi m’mene zinthu zikuyendera m’dziko muno kuphatikiza kusowa kwa mafuta komanso kufuna kuti bungwe loyendetsa zisankho la MEC libwele poyera kufotokozera bwino za m’mene likugwilira ntchito yake yokonzekelera zisankho za pa 16 September 2025.

Anthu ambiri komanso akatswiri oyankhula pa za kayendetsedwe ka dziko adandaula ndi m’chitidwe omwe wayamba kumela nthenje m’dziko muno, omaopseza ndi zikwanje anthu omwe akufuna kupanga zionetselo zosakondwa ndi m’mene zinthu zikuyendera kapena zomwe zikuwaphinja.

Advertisement