Musachite ziwonetsero mawa, a Polisi akhala otangwanika – Boma liuza Namiwa

Advertisement
Sylvester Namiwa

Boma, komanso akuluakulu a polisi apempha wamkulu wa bungwe la CDEDI a Slyvester Namiwa kuti ziwonetsero zomwe akonza kuti zichitike lachinayi pa 21, November asachite kamba koti a polisi akhala otangwanika.

Iwo apempha a Namiwa ndi azinzawo kuti achite ziwonetserozi lolemba sabata la mawa.

Malinga ndi akuluakulu a polisi, mawa a polisi achitetezo akhala otangwanidwa kuperekeza mtsogoleri wa dziko lino ku Bunda komwe ali ndi zochita.

A Namiwa awapemphanso kuti asinthe njira yogwilitsa ntchito tsiku la ziwonetsero likafika.

Ziwonetserozi zinakonzedwa pofuna kukakamiza nkulu wa bungwe la MERA komanso Ibrahim Matola nduna yazamphavu kutula pansi udindo kamba kolephera kugwira ntchito maka pa nkhani ya mafuta.

Mkulu wa bungwe la la CDEDI a Sylvester Namiwa agwilizana ndi pemphori, ndipo wawuza akuluakulu a Boma kuti pofika lolemba asabwerenso ndi zifukwa dzina.

Advertisement