Sitikutula pansi udindo – wanenetsa Mtalimanja

Advertisement
MEC

Wapampando wabungwe loyendetsa zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) a Annabel Mtalimanja, atemetsa nkhwangwa pa mwala kuti iwo pamodzi ndi mkulu ku bungweli a Andrew Mpesi satula pansi maudindo awo.

Izi zikudza pomwe mabungwe ena komanso zipani zina zotsutsa boma zakhala zikuuza a Mtalimanja ndi a Mpesi kuti atule pansi maudindo awo posasangalatsidwa ndi kagwilidwe kawo ka ntchito.

Mwazina, mbali zodandaulazi zikuloza chala a Mtalimanja komaso a Mpesi kuti ndi otsatira chipani cholamula cha Malawi Congress (MCP) zomwe akuti zitha kudzakhudza zisankho za chaka cha mawa.

Koma poyankhula kwa atolankhani pakutha pamkumano omwe MEC inachititsa ndi atsogoleri azipembedzo, Mtalimanja wanenetsa kuti iye pamodzi ndi a Mpesi sagonjera pempho la mabungwe komanso zipani zotsutsa bomazi.

A Mtalimanja ati palibe lamulo lili lonse lomwe lidaphwanyidwa pa kusankhidwa kwawo kukhala paudindowu, ndipo walangiza onse omwe akudandaula kuti atsate ndondomeko zoyenera zofuna kuthetsera nkhawa zawo.

Pa nkhani ya kampani ya Smartmatic, Mtalimanja wati bungwe la MEC linatsata ndondomeko zoyenera ndipo zipani zonse zinagwira nawo ntchito yosaka kampani yoti idzagwire ntchito ya zisankhoyi.

Pakadali pano, mbali zonse zokhudzidwa zomwe zikukakamiza a Mtalimanja komaso a Mpesi kutula pansi maudindo awo, sizinabwele poyera ndikupeleka zomwe zichite potsatira kukana kutula pansi udindoku.

Advertisement