Masewero ofuna kupeza katswiri wa kickboxing aliko mawa

Advertisement
Zomba

Bungwe la Malawi Kickboxing Association (MAKBA) lakonza masewero ofuna kupeza akatswiri amasewerowa kuno ku Malawi omwe adzachitike Lamulungu ku Chinamwali Complex mu mzinda wa Zomba.

Mlembi wamkulu wa Bungwelo a Bright Limani ati akatswiri 55 ochokera m’ma Kickboxing Club a Bangwe, Cobbe Barracks, Nyambadwe, Bvumbwe, Thondwe, Mangochi, Mzuzu, Chinamwali, Kachere, Real Fitness, Tianjin, BYC, ndiwomwe awonetsa chidwi ofuna kudzachita nawo mpikisanowu.

A Limani ati mpikisanowu ndi wachitatu kuchitika kuti ma kalabu ochokera mzigawo zonse a kickboxing amuno M’malawi chikhazikitsidwileni m’chaka cha 2020.

“Tili ndichikhulupiliro kuti anthu adzabwera kudzawonera masewero amenewa Lamulungu ku Chinamwali Complex komwe akatswiri a Flyweight, Bantamweight, Middleweight, Lightweight ndi Heavyweight ankamenyane mwa mtima bii,” adatero a Bright Limani.

Iwo apempha anthu okhala madera a Chinamwali, Matawale, Chikanda, Mpunga, Sadzi, 3 Miles, Old Naisi kuti adzafike ndi mabanja awo kuti azasangalale ndipo alonjeza kuti chitetedzo chikakhalako chokwanira

Pamenepa, mlembiyu wati masewerowo akuyembekezeka kukasankha akatswri omwe akayimire dziko la Malawi kumpikisano wa African Kickboxing Championships omwe uzachitikire m’dziko la South Africa mu December chaka chino cha 2024.

Advertisement