Sindidabweretse njala m’dziko muno – Chakwera

Advertisement
Chakwera

Mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera wati njala yomwe ili m’dziko muno sadabweretse ndi iye koma zifukwa zomwe zachititsa kuti zokolora zichepe mlimi aliyense akuzidziwa.

A Chakwera anayankhula izi pamene amatsegulira ndondomeko ya zipangizo zotsika mtengo ya Affordable Inputs Program (AIP) ku Neno.

Iwo anati pofuna kuthana ndi mavuto a njala m’dziko muno, boma likupereka chakudya kwa anthu kudzera ku Nthambi ya DoDMA.

Mtsogoleriyu anapitiliza kunena kuti aMalawi asanamizidwe kuti iye sakuwachitila kanthu kamba koti kabwino kalikonse akupeza kakuchokera muzomwe iye akuchitira aMalawi m’dziko muno.

“Ngati kudera kwa m’Malawi aliyense kukuchitika chitukuko chomwe chathandiza kuti aMalawi ena apeze ntchito, wina asakunamizeni kuti Chakwera sadakuchitireni kalikonse ayi,” adatero aChakwera.

Iwo adatinso aMalawi asayang’ane mbali imodzi yazinthu kamba koti boma lake likuchita zinthu zosiyanasiyana zomwe zikupindulira aMalawi onse.

Polankhula Nduna ya Zaulimi, a Sam Kawale ati, chaka chino malo 597 akhazikitsidwa kuti anthu adzikagula fetereza komanso pali misika ina yomwe anthu azigula fetereza kufupi ndi kumene akukhala.

A Kawale anatinso zambiri ziyenda bwino mundondomekoyi kamba koti zotsamwitsa za chaka chatha zakonzedwa ndipo nawo a Zanyengo ati mvula igwa bwino chaka chino.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.