Chiwerengero cha anthu otenga matenda opatsirana pogonana chakwera

Advertisement
Mzimba

Akatswiri a za umoyo dera la kum’mwera kwa boma la Mzimba ati chiwengero cha achinyamata omwe akutenga matenda opatsirana pogonana chikunka nakwera tsiku ndi tsiku.

Malingana ndi yemwe akuyang’anira zamatenda opatsirana pogonana pa chipatala cha boma la Mzimba a Dan Kwacha wati ndizodetsa nkhawa kuwona kuti akugawa makondomu ambiri koma anthu ambiri akutengabe matenda opatsiranawa tsiku ndi tsiku. 

Kwacha wati pakati pa mwezi wa June kufika September anthu opitilira 2,800 atenga matendawa.

“Monga chipatala, ndife odabwa komanso tili ndi nkhawa kuona anthu ambiri akutenga matendawa angakhale kuti ife tikuyetsetsa kulimbikitsa anthu kuti azigwiritsira ntchito makondomu kuti apewe kutenga matenda omwe amadza kamba kogonana,” watero Kwacha.

Iye watinso angakhale kuti chiwerengero cha omwe akutenga matendawa chikukwera, iwo ngati aza umoyo ndi okondwa kuti anthuwa akumafika kuchipatala ndi kulandira thandizo loyenera.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.