Pamene mabungwe ndi anthu akulimbikitsa atsikana kupititsa luso lawo patsogolo, m’boma la Mzimba muli mtsikana wina yemwe dzina lake ndi Trancy Chapweteka yemwe ali ndi luso lolemba nkhani komanso ndakatulo koma akusowa thandizo kuti lusoli lipite chitsogolo.
“Ndili luso lolemba nkhani zosiyanasiyana kuphatikizapo ndakatulo,ndipo ndikufuna thandizo kuti luso langali lipite patsogolo, ine abambo anga anamwalira ndili wang’ono kwambiri ndipo ndakula ndi Mai anga movutika,” iye anatero.
Iye wati anthu akufuna kwabwino atha kumuthandiza ndi Laptop yoti adzitha kugwiritsa ntchito polemba nkhani komanso ndakatulo.
Iye watinso akufunitsitsa kwambiri kuti zomwe akulemba zidziwike dziko lonse ndipo akupempha nyumba zoulutsa ndi kutsindika mawu kumuthandiza popititsa patsogolo luso lake.
Iye wayamikira Malawi24 pomuyendera ndikumulimbikitsa.
“Ndithokoze Malawi24 ponditsatira ndipo ndili nacho chikulupiriro kuti nkhani yanga anthu akaiona athandiza ndithu,” anapitiliza kufotokoza.
Trancy wati amene akufuna kumuthandiza alumikizane ndi mtolankhani wa Malawi24 Ephraim Mkali Banda pa ma nambala awa 0993594211kapena 0887301555
Trancy analemba mayeso ake a fomu 4 chaka chatha pa sukulu ya secondary