Matako apatsidwa chilango chogwira ntchito zosalipidwa 

Advertisement
Matako

Bwalo la Senior Resident Magistrate Joshua Nkhono ku Balaka lalamula kuti a Lilian Matako komanso a Ishmael Chitete akagwire ntchito zosalipidwa m’dera lawo atapezeka olakwa pa mlandu ovulaza munthu mwadala.

Awiriwa adamangidwa zitadziwika kuti adapeleka chilango chomumangilira mumtengo mwana wa zaka zisanu ndi zinayi, Mercy Magombo, komanso kumuthira madzi a chitedze kaamba komuganizira kuti adaba ndalama yokwana K2,000 ya a Matako, omwe ndi Mai ake a mwanayu.

Poyambilira, oweruza mlandu a Joshua Nkhono adalamula kuti awiriwa akagwire ntchito ya kalavulagaga ku ndende kwa chaka chimodzi.

Komabe, chilango cha awiriwa chidachepetsedwa ndipo oweruza mlandu adalamula kuti anthuwa akagwire ntchito za zosalipidwa monga kusesa komanso kukolopa ku polisi ya Balaka komanso ma ofesi ena a khonsolo ya boma la Balaka kwa maola okwana 480.

A Nkhono adati adapereka chilango chimenechi kaamba koti mai Matako amasamalira okha ana awo komanso aka ndi koyamba kuti anthu awiriwa apalamule mlandu kuphatikinzanso kuti adavomera za kulakwa kwawo.

Advertisement